NOVEMBER 29, 2019
AUSTRALIA
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Melbourne, Australia
Masiku: 22 mpaka 24 November, 2019
Malo: Marvel Stadium ku Melbourne, Australia
Zinenero: Chinenero Chamanja cha ku Australia, Chitchainizi cha Chikantonizi, Chitchainizi cha Chimandarini, Chingelezi, Chikoleya, Chisipanishi, Chitagalogi ndi Chivetinamu
Chiwerengero cha Osonkhana: 46,582
Chiwerengero cha Obatizidwa: 407
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,083
Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Canada, Hong Kong, India, Italy, Japan, Korea, Philippines, Solomon Islands, South Africa, Taiwan, ndi United States
Zina Zomwe Zinachitika: Bwana wa ku Ballarat Wildlife Park anati: “Kunena moona mtima, pa zaka 15 zomwe ndakhala ndikugwira ntchito ku Ballarat Wildlife Park, gulu lanu limachita zinthu mwadongosolo kwambiri poyerekeza ndi magulu ena omwe ndagwira nawo ntchito. Zikomo kwambiri nonsenu kuphatikizapo omwe ayendetsa dongosolo la maulendo anu.”
Bwana wina anayamikira alendo 340 omwe anagona mu hotelo yake. Iye anati: “Anthu onse ankalankhulana bwino kwambiri pokambirana mmene angakonzere zinthu. Ndikungoona ngati kuti ndinu anthu a m’banja limodzi lalikulu ndipo nonse mukulankhulana bwino ndi kuthandizana. Ndinene motsimikiza kuti ndasangalala kwambiri kugwira nanu ntchito. Ndakhala ndikugwira ntchito yosamalira alendo kwa zaka 11 ndipo ndi gulu lanu lokha limene lachita zinthu moteremu.” Bwanayu ataona mmene a Mboni za Yehova ankachitira zinthu, anapezeka pamsonkhano tsiku Loweruka.
Abale ndi alongo akulandira alendo ochokera kumayiko ena ku ofesi ya nthambi yomwe ili m’dera la Denham Court ku Australia
Abale ndi alongo akufika pamalo a msonkhano
Alendo ochokera kumayiko ena akuimba nawo nyimbo zotamanda Yehova
Mlongo wachitsikana akukumbatira amayi ake atabatizidwa
M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lachisanu
Alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera akweza manja m’mwamba polonjera gulu la anthu
Alendo akujambulana
Pa zochitika zamadzulo, alongo akuvina posangalatsa alendo