Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 6, 2017
AUSTRALIA

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Tropical Cyclone Debbie Inawononga Zinthu ku Australia

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Tropical Cyclone Debbie Inawononga Zinthu ku Australia

Pa 28 March , 2017, kunachitika mphepo yamkuntho kumpoto kwa madera a m’mbali mwa nyanja ku Queensland komanso zilumba zina zapafupi, yotchedwa Tropical Cyclone Debbie. Mphepoyi inkathamanga liwiro la makilomita 260 pa ola. Mphepoyi inagwetsa mitengo, inawononga nyumba, komanso inaphwanya maboti omwe anali m’matawuni a m’mbali mwa nyanja. Inachititsanso kuti madzi asefukire m’mizinda ndi m’matawuni a kum’mwera kwa Queensland komanso kumpoto kwa New South Wales, ndipo izi zinachititsa kuti anthu ambiri akhale opanda magetsi.

Malipoti amene anaperekedwa poyamba ankasonyeza kuti palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene anavulala kwambiri kapena kufa. Komabe, mphepoyi inawononga nyumba zambiri za a Mboni ndipo inagwetseratu imodzi mwa nyumbazo. Nyumba za Ufumu ziwiri (kapena kuti malo olambirira) nazonso zinawonongeka.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Australia inakhazikitsa makomiti awiri opereka thandizo. Makomitiwa amapereka majenereta, chakudya komanso madzi kwa anthu a m’madera amene anakhudzidwawo. A Mboni amene sanakhudzidwe ndi mphepoyi akuthandiza anzawo amene akhudzidwa kuti asamangoganizira zimene zawachitikirazo ndiponso akuwathandiza mwauzimu.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi limene limayendetsa ntchito yopereka thandizo kwa anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi. Iwo amachita zimenezi kuchokera kulikulu lawo padziko lonse ndipo amagwiritsa ntchito ndalama zothandizira pantchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova zimene anthu amapereka.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Australasia: Rodney Spinks, +61-2-9829-5600