Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 7, 2015
AUSTRIA

Chikwangwani Chachikumbutso Chinaikidwa Pokumbukira wa Mboni Amene Anaphedwa ndi a Chipani cha Nazi

Chikwangwani Chachikumbutso Chinaikidwa Pokumbukira wa Mboni Amene Anaphedwa ndi a Chipani cha Nazi

Gabriele Votava, yemwe ndi meya wa dera lina la mumzinda wa Vienna, akulankhula pa nthawi yoonetsa chikwangwanicho

VIENNA, ku Austria—Pa 13 May 2015 anthu 400 anapezeka pamwambo wokumbukira Gerhard Steinacher yemwe anali wa Mboni za Yehova. Gerhard anaphedwa zaka 75 zapitazo ndi a chipani cha Nazi chifukwa chokana kulowa m’gulu la asilikali a ku Germany. Meya wa dera lina la mumzinda wa Vienna dzina lake Gabriele Votava, anali mlendo wolemekezeka pamwambo woonetsa anthu chikwangwani chimene chinaikidwa panyumba imene banja la a Steinacher linkakhala mumzinda wa Vienna.

Mutu wa mwambowu unali wakuti, “Sindingawombere.” Gerhard ndi amene ananena mawu amenewa pa nthawi imene ankapempha kuti asalowe usilikali. Mawu osavutawa amasonyeza mfundo zachikhristu zimene Gerhard ankatsatira. Iye ankamvera mawu a Yesu a pa Mateyu 19:19 akuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”

Gerhard ali mwana ankakonda kuwerenga Baibulo ndipo atafika zaka 17, anakhala wa Mboni za Yehova. Pa 15 September 1939, anamangidwa chifukwa choti anakana usilikali komanso anakana kulumbira kuti akhala okhulupirika kwa Hitler. Gerhard atakhala mundende kwa milungu 6 ku Vienna, anamusamutsa n’kumupititsa kundende ina ya mumzinda wa Berlin, ku Germany.

Mu 1976 mayi ake a Gerhard atamwalira, bokosi lokhala ndi makalata ndi makhadili linapezeka m’nyumba yawo.

Pa 11 November 1939, tsiku loyamba kuzenga mlanduwu, khoti linagamula kuti Gerhard ali ndi mlandu wokana kuthandiza pa nkhondo ndipo akuyenera kuphedwa. Iye anapempha kuti amumvere chisoni chifukwa chakuti ankakana usilikaliwo chifukwa cha zimene amakhulupirira. Komabe pa 2 March 1940, khoti la asilikali linavomera kuti Gerhard ayenera kuphedwa. Patadutsa milungu inayi, pa 30 March, Gerhard anaphedwa mochita kudulidwa mutu kundende ina ya ku Berlin. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 19 zokha.

Ataonetsa chikwangwani chija, anapita kuholo ina kuti akapitirize mwambowo. Kumeneko anaonetsa zinthu zina zokhudza mbiri ya banja la a Steinacher. Pa zinthu zimene anaonetsa panali kabokosi komwe munali makalata 28 amene makolo a Gerhard Steinacher anamulembera pamene anali m’ndende. Munalinso makhadi ndiponso makalata 25 omwe Gerhard analembera makolo ake kuti awalimbikitse ndiponso kuwatsimikizira kuti adakali ndi chikhulupiriro cholimba.

Nyuzipepala ina ya ku Vienna inanena kuti “mwambowo unali wabwino kwambiri” ndipo unathandiza kuti “anthu onse adziwe” za kulimba mtima kwa Gerhard. Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “[Gerhard] anali wokonzeka kufera mfundo zimene ankatsatira pa moyo wake.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Austria: Johann Zimmermann, tel. +43 1 804 53 45

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110