JULY 21, 2014
AUSTRIA
A Mboni za Yehova Analandira Ulemu Pamwambo Wokumbukira Anthu Amene Anazunzidwa M’ndende ya Gusen
SELTERS, Germany—Lamlungu, pa April 13, 2014, pamwambo wokumbukira anthu amene anazunzidwa m’ndende ya Gusen ku Austria, anaika chipilala pokumbukira anthu 450 a Mboni za Yehova amene anamangidwa mu ulamuliro wa chipani cha Nazi kundende ya Mauthausen ndi ya Gusen. Alendo oposa 130 anapezeka pamwambowu.
A Mboni atafika kundende ya Mauthausen, msilikali woyang’anira ndendeyo anawaopseza kuti: “Palibe wa Mboni amene atuluke muno wamoyo.” Martin Poetzinger, yemwe anapulumuka pambuyo pokhala zaka 9 m’ndende za Dachau, Mauthausen, ndi Gusen yemwe kenako anadzakhala membala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mumzinda wa New York, ananena zimene zinamuchitikira ali kundende ya Mauthausen. Iye anati: “Asilikali anachita zonse zimene akanatha pofuna kuwononga chikhulupiriro chathu.””
Patapita nthawi, a Mboni ena amene anali kundende ya Mauthausen anasamutsidwira kundende ya Gusen. Cholinga cha ndendeyi kunali kupherako anthu moti tsiku ndi tsiku anthu ankaphedwa. A Mboni ankakumana m’timagulu usiku kuti akambirane nkhani za m’Baibulo zimene anaziloweza. Ankachita izi kuti alimbitse chikhulupiriro chawo. Nthawi ina anapeza Baibulo lomwe linagawidwa m’mbali zosiyanasiyana ndipo ankawerenga mosinthanasinthana. Ankabisa Baibuloli pansi pa mabedi awo ndipo ankaliwerenga nthawi iliyonse imene apeza kampata.
A Mboni ankauzanso ena mobisa uthenga wa m’Baibulo. Akaidi 5 a ku Poland anaphunzira Baibulo ndi a Mboni ndipo anabatizidwa mobisa mu kadamu kamatabwa kamene a Mboniwa anakapanga kuti azibatiziramo anthu. Bambo Franz Desch omwenso ndi a Mboni ankaphunzira Baibulo ndi wapolisi ndipo kenako nayenso anakhala wa Mboni za Yehova.
Bambo Wolfram Slupina, womwe amalankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Austria, ananena kuti: “Tikuthokoza kwambiri kuti a Mboni akukumbukiridwa chifukwa cha chikhulupiriro komanso kulimba mtima kumene anakusonyeza nthawi imene anali m’ndende za Mauthausen ndi Gusen. Iwo anayesetsa kusonyeza makhalidwe Achikhristu monga chifundo ndi kukoma mtima ngakhale kuti ankazunzidwa. Zimene anachitazi n’zoyeneradi kuzikumbukira komanso kuzitsanzira.
Kuchokera m’mayiko ena:
Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Austria: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110