Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 29, 2020
AZERBAIJAN

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lapereka Zigamulo Ziwiri Zokomera Mboni za Yehova ku Azerbaijan

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lapereka Zigamulo Ziwiri Zokomera Mboni za Yehova ku Azerbaijan

Pa 24 September 2020, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka zigamulo ziwiri zofunika kwambiri zokomera a Mboni za Yehova ku Azerbaijan. Chigamulo choyamba chinali chokhudza mlandu wa Valiyev and Others v. Azerbaijan, ndipo chachiwiri chinali cha mlandu wa Religious Community of Jehovah’s Witnesses v. Azerbaijan. Zigamulo ziwirizi zilimbikitsa ufulu wa abale athu woti azitha kulambira momasuka.

Pa milandu iwiri yonseyi, boma la Azerbaijan linavomera kuti linaphwanya ufulu wa abale athu. Bomali linavomeranso kupatsa abale athu chipukuta misozi cha ndalama zokwana madola 22,146 a ku America. Zigamulo za khoti la ECHR zikusonyeza kuti khotili linagwirizana ndi zimene boma la Azerbaijan linanena zoti linaphwanya ufulu wa abale athu.

M’bale Valiyev akuchititsa msonkhano m’nyumba ya m’bale wina

Mlandu wa Valiyev and Others v. Azerbaijan, womwe unapita ku khoti la ECHR mu 2011, unali wokhudza abale athu mumzinda wa Ganja. Kwa zaka zambiri akuluakulu a boma ku Ganja anakhala akuletsa gulu lathu kulembetsa kuti likhale lovomerezeka kuboma. Chifukwa cha zimenezi apolisi akhala akusokoneza misonkhano yathu yomwe imachitika mwamtendere, kumanga aliyense amene wapezeka pamisonkhanoyo komanso kuwalipiritsa chindapusa cha ndalama zambiri. M’bale wina anamangidwa ndi kulipiritsidwa chindapusa maulendo ambirimbiri. Pamapeto pake ndalama zonse zimene anapereka zinakwana madola 11,375 a ku America. Abale ndi alongo ena mpaka anaikidwa m’ndende chifukwa sakanakwanitsa kulipira chindapusa cha ndalama zambiri chonchi.

Mu 2013 abale anapititsa ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe mlandu wina wakuti Religious Community of Jehovah’s Witnesses v. Azerbaijan, chifukwa dziko la Azerbaijan linachepetsa chiwerengero cha mabuku chimene abalewa angathe kulowetsa m’dzikolo.

Ngakhale kuti boma silinapereke chilolezo chakuti abale athu angathe kulembetsa gulu lathu ku Ganja, panopa zinthu ziliko bwino. Tikutero chifukwa chakuti m’zaka zaposachedwapa abale athu akhala akusonkhana m’magulu ochepa m’nyumba za abale popanda kusokonezedwa ndi apolisi. Komanso boma linavomereza kuti abale athu azitha kuitanitsa mabuku okwanira ngakhale kuti limafunika kuona kaye mabukuwa asanaitanitsidwe.

M’bale Kiril Stepanov, yemwe amagwira ntchito mu Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Azerbaijan ananena kuti: “Tikukhulupirira kuti chigamulo chimene khoti la ECHR lapereka, chithandiza kuti gulu lathu lilembetse mwamsanga kuboma kuti likhale lovomerezeka mumzinda wa Ganja komanso m’mizinda ina ya ku Azerbaijan. Tikukhulupiriranso kuti m’tsogolo muno boma lidzasiya kumaona kaye mabuku amene tikufuna kuitanitsa.”

Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chotithandiza. Zigamulo zotikomerazi zikupereka umboni winanso wakuti ‘palibe chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chivulaze anthu a Mulungu chomwe chidzapambane.’—Yesaya 54:17.