Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 28, 2021
AZERBAIJAN

Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu Yagamula Mokomera a Mboni za Yehova

Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu Yagamula Mokomera a Mboni za Yehova

Pa 26 April 2021, Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapereka chigamulo chosaiwalika pa mlandu wokhudza a Mboni za Yehova ku Azerbaijan (Aziz Aliyev and Others v. Azerbaijan). Aka ndi kachitatu kuti komitiyi ipereke chigamulo chokomera a Mboni za Yehova m’dziko la Azerbaijan ndipo chigamulochi chateteza ufulu wathu wolambira mwamtendere.

Mlanduwu ndi wokhudza zimene apolisi anachita m’dera lina lotchedwa Aliabad m’chigawo cha Zagatala. Pa 21 September 2013, apolisi anakathyola m’nyumba ya M’bale Aziz Aliyev mosatsatira malamulo. Pa nthawiyi, a Mboni za Yehova ambiri anali akuchita misonkhano yawo ya mpingo m’nyumbayi. Apolisiwo anachita chipikisheni ndipo anawopseza abale ndi alongo, anawalanda mabuku awo, ziphaso zawo zaboma ndi zakuchipatala komanso anawalanda ndalama. Kenako anawatenga onsewo n’kupita nawo kupolisi. Ali m’njira, Mlongo Havva Azizova anayamba kudwala n’kukomoka. Apolisiwo ataona zimenezi, anamutengera kuchipatala. Atangodzidzimuka, anamutenga n’kupita naye kupolisi kuti akamufunse mafunso.

Kenako, Khoti la m’Boma la Zagatala linagamula kuti ambiri mwa abale ndi alongowa alipire chindapusa cha ndalama zomwe pa nthawiyo zinakwana $1,716. Khoti la Apilo la Sheki linagwirizana ndi chigamulo cha khoti loyamba lija. Abale ndi alongowa anachita zonse zomwe akanatha kuti achite apilo chigamulochi m’dziko la Azerbaijan koma zinakanika. Ndiyeno anakachita apilo ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu.

Komitiyi inagamula kuti dziko la Azerbaijan linaphwanya ufulu wachipembedzo ndiponso linamanga komanso kuzunza abalewa mosatsatira malamulo. Komitiyi inanena kuti a Mboni za Yehova anachitiridwa nkhanza ndi apolisi komanso akuluakulu ena omwe anawaopseza kuti “awatsekera m’ndende, ananyoza ena mwa a Mboniwo ndiponso analankhula zinthu zotsutsa chipembedzo chawo koma sanafotokoze mmene misonkhano yawo kapena mabuku a chipembedzo chawo zinasokonezera kapena kuika moyo wa anthu ena pachiopsezo.” Chifukwa cha zimenezi, dziko la Azerbaijan linapemphedwa kuti lipereke chipukuta misozi kwa abale athuwa ndipo “lichite zonse zofunikira poonetsetsa kuti zimene zinachitikazi zisadzachitikenso m’tsogolomu komanso liunikenso malamulo ake okhudza nkhaniyi.”

Ndife osangalala kwambiri kuti panopa abale athu ku Azerbaijan aloledwa kuti azilambira komanso kusonkhana mwaufulu. Tikuthokoza Mulungu wathu Yehova chifukwa akutithandiza kuti choonadi chipitirizebe kukhazikitsidwa mwalamulo m’makhoti amasiku ano.—Afilipi 1:7.