Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 24, 2018
AZERBAIJAN

Dziko la Azerbaijan Lagamula Kuti M’bale Wathu Wina Ndi Wolakwa Chifukwa Chokana Kulowa Usilikali

Dziko la Azerbaijan Lagamula Kuti M’bale Wathu Wina Ndi Wolakwa Chifukwa Chokana Kulowa Usilikali

Pa 6 July, 2018, khoti la m’boma la Barda ku Azerbaijan, linapereka chilango kwa Emil Mehdiyev wazaka 18 yemwe ndi wa Mboni za Yehova ndipo anapatsidwa malamulo oti azitsatira kwa chaka chimodzi kuti asaikidwe m’ndende. Khotili linanena kuti Emil ndi wolakwa chifukwa chokana kulowa usilikali, koma silinagamule kuti akakhale m’ndende. Ngakhale zili choncho Emil sangasamukire m’dera lina popanda kudziwitsa kaye apolisi ndipo sakuloledwa kutuluka m’dziko la Azerbaijan.

Mu December 2017, M’bale Mehdiyev anaitanidwa kuti apite ku dipatimenti ya m’dera la Barda yomwe imalemba anthu usilikali komanso imauza asilikali zoyenera kuchita. (Barda District Department of the State Service for Mobilization and Conscription) Iye anakana kusaina chikalata chosonyeza kuti akulowa usilikali chifukwa chikumbumtima chake sichingamulole kugwira ntchitoyi. Atalamulidwa kuti alowe ntchito yausilikali, iye anafotokoza zomwe amakhulupirira ndipo anapempha kuti apatsidwe ntchito ina m’malo mwa usilikali. Koma anauzidwa kuti mwayi umenewo palibe ndiponso kuti nkhani yakeyo aitumiza ku ofesi ya woimira boma pa milandu m’boma la Barda.

Pambuyo pozenga mlanduwu maulendo angapo, khoti la m’boma la Barda linagamula kuti Emil wapezeka wolakwa ndipo linalamula kuti apatsidwe chilango komanso anapatsidwa malamulo oti azitsatira. Ngakhale kuti khotili silinagamule kuti Emil akakhale m’ndende, panopa akuonedwa ngati munthu yemwe anapalamula mlandu ndipo palibe chilichonse chimene angachite chifukwa boma la Azerbaijan silinakhazikitsebe lamulo loti anthu atha kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali, monga mmene lakhala likulonjezera kwa nthawi yayitali.

Ndife osangalala kuti M’bale Mehdiyev sanasinthe maganizo ake pa nkhaniyi ngakhale kuti akukumana ndi mavuto.—1 Petulo 2:19.