Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 8, 2018
AZERBAIJAN

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Azerbaijan Lavomereza Kuti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova Apatsidwe Chipepeso

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Azerbaijan Lavomereza Kuti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova Apatsidwe Chipepeso

Pa 16 April, 2018, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Azerbaijan linavomereza chigamulo chomwe khoti laling’ono linapanga choti a Irina Zakharchenko ndi a Valida Jabrayilova apatsidwe chipepeso chifukwa anatsekeredwa m’ndende kwa miyezi 11 mopanda chilungamo. M’mbuyomu mu February 2017, Khoti Lalikulu Kwambiri linapeza kuti azimayiwa si olakwa pa mlandu womwe ankaimbidwa woti ankagawira mabuku achipembedzo popanda kupempha chilolezo ku boma. Komabe khotili linasiya nkhani yopereka chipepesoyi m’manja mwa makhoti ang’onoang’ono.

Atapezeka kuti si olakwa, a Zakharchenko ndi a Jabrayilova omwe ndi a Mboni za Yehova, anakapempha ku makhoti ang’onoang’ono kuti apatsidwe chipepeso chifukwa cha nkhanza zomwe anachitidwa. Mu August 2017, khoti la mumzinda wina linagamula kuti apatsidwe chipepeso koma a Unduna wa Zachuma anachita apilo za chigamulochi. Ndiyeno mu November 2017, khoti la apilo linavomereza chigamulo chomwe khoti la mumzinda wina uja linapanga. A Unduna wa Zachuma sanagwirizane nazobe ndipo anakadandaula ku Khoti Lalikulu Kwambiri mu February 2018. Koma Khoti Lalikulu Kwambiri linakana apilo imeneyi ndipo linavomereza chigamulo choti azimayi awiriwa apatsidwe chipepeso.

Khoti Lalikululi litagamula zoti azimayiwa apatsidwe chipepeso, linanenanso kuti likudziwa nkhanza zomwe akuluakulu a boma anachitira a Zakharchenko ndi a Jabrayilova ndipo anagwiritsa ntchito udindo wawo molakwika komanso anaphwanya ufulu wa azimayi osalakwawa.