Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 22, 2018
AZERBAIJAN

Boma la Azerbaijan Lalemba Chipembedzo cha Mboni za Yehova Kukhala Chovomerezeka ku Baku

Boma la Azerbaijan Lalemba Chipembedzo cha Mboni za Yehova Kukhala Chovomerezeka ku Baku

Pa 8 November, 2018, komiti ya boma ku Azerbaijan komwe zipembedzo zimakalembetsako kuti zikhale zovomerezeka, inavomereza kuti a Mboni za Yehova alembetse chipembedzo chawo ku Baku, lomwe ndi likulu la Azerbaijan. Panopa abale athu ndi otetezeka kwambiri ndi malamulo kuti akhoza kumalambira komanso kulalikira mwaufulu mumzindawo.

Tikukhulupirira kuti zimene komitiyi yachita zithandiza kuti abale athu m’madera ena a dzikoli athe kulembetsanso n’kukhala ovomerezeka ndi malamulo. Tikuthokoza Yehova kuti akuluakulu a boma a mtima wabwino akhazikitsa mwalamulo chipembedzo chathu ku Baku.—Afilipi 1:7.