Pitani ku nkhani yake

MAY 26, 2014
AZERBAIJAN

A Mboni za Yehova ku Azerbaijan Adandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Pofuna Kuti Bomalo Lizilemekeza Ufulu Wawo Wolambira

A Mboni za Yehova ku Azerbaijan Adandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Pofuna Kuti Bomalo Lizilemekeza Ufulu Wawo Wolambira

Tsiku lina Lamlungu m’mawa m’dera la Baku m’dziko la Azerbaijan, amuna, akazi komanso ana pafupifupi 200 omwe ndi a Mboni za Yehova, anasonkhana m’chipinda china n’kumamvetsera nkhani ya m’Baibulo.

Mwadzidzidzi apolisi analowa m’chipindamo. Iwo anali ndi akuluakulu ena aboma ndiponso anthu ena amene anali ndi makamera a TV. Apolisiwa anasokoneza msonkhano wa anthu a Mboniwa ndiponso anamenya amuna ambiri amene anali m’chipindacho. Iwo anayamba kufufuza mopanda chilolezo m’chipindamo. Kenako anayamba kunyoza anthu amene anasonkhana m’chipindacho ndipo analanda ndalama, makompyuta ndi mabuku othandiza pophunzira Baibulo. Apolisiwo anagwira anthu ambiri a Mboniwo n’kukawatsekera kwa maola ochuluka ndithu. A Mboni enanso omwe anali ochokera m’mayiko akunja, anatsekeredwa kwa masiku angapo, kenako anawathamangitsa m’dzikolo. Ndipo TV ya m’dzikoli inaulutsa nkhani yoipitsa mbiri ya Mboni za Yehova pofotokoza zimene apolisi anachita pamene ankasokoneza msonkhano uja.

Nkhaniyi inachitika pa December 24, 2006, ndipo zinachititsa kuti a Mboni za Yehova akadandaule koyamba ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya chifukwa cha zimene boma la Azerbaijan linawachitira. Kuyambira nthawi imeneyi, a Mboni za Yehova adandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, pa milandu yokwana 18, chifukwa choti anaphwanyiridwa ufulu wawo wolambira.

ZIMENE ZACHITITSA KUTI ADANDAULE KUKHOTI

ZONSE

Kuzunzidwa ndi Apolisi

5

Kulembetsa Kachiwiri

1

Kuchita Zinthu Zogwirizana ndi Chipembedzo

2

Kuunika Zonse Zimene Zili M’mabuku Athu

5

Kuthamangitsa Anthu a M’mayiko Ena

3

Kukana Kuchita Zinthu Zosagwirizana ndi Zimene Amakhulupirira

3

Zonse

19

Kuchuluka kwa milandu imene a Mboni anasumira boma la Azerbaijan ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu, pofika pa January 31, 2014

Taonani zitsanzo za zinthu zimene zinachititsa a Mboni za Yehova kukadandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya chifukwa cha zimene boma la Azerbaijan likuwachitira.

  • Boma Likukana Kulembanso Chipembedzo cha a Mboni

    A Mboni za Yehova analembetsa ku boma chipembedzo chawo koyamba pa December 22, 1999, m’dera la Baku. Kenako iwo analembetsanso chipembedzochi pa February 7, 2002 ku bungwe la boma loona za zipembedzo. Mu 2009, boma la Azerbaijan linasintha malamulo ake okhudzana ndi ufulu wolambira, ndipo zimenezi zinachititsa kuti zipembedzo zonse m’dzikoli zilembetsedwenso. A Mboni za Yehova anakapereka kuboma zikalata zolembetsera chipembedzo chawo, koma bomalo linakana pa zifukwa zosamveka bwinobwino. Mogwirizana ndi malamulo, mu 2002 boma linalemba m’kaundula Mboni za Yehova kukhala chipembedzo chovomerezeka. Ngakhale kuti bomalo silinasinthe zimenezi, panopa likukana zoti a Mboniwo alembedwenso m’kaundula mogwirizana ndi malamulo atsopano okhudza zipembedzo.

  • Nkhanza Zimene Apolisi Akuchita

    Ku Azerbaijan, mlungu uliwonse a Mboni za Yehova amasonkhana m’nyumba za anthu osiyanasiyana a chipembedzochi n’kumalambira Mulungu. Nthawi zambiri, apolisi amalowa m’nyumbazi popanda chilolezo n’kusokoneza misonkhano yawo. Apolisi amazunza a Mboniwo ndipo amawatsekera kupolisi kwa maola ambiri. Komanso amawalanda mabuku amene amagwiritsa ntchito polambira Mulungu. Ndipo a Mboni ena amawalipiritsa chindapusa cha ndalama zambirimbiri. Mwachitsanzo, mu 2011 anthu 6 a Mboni m’dera la Ganja analamulidwa kupereka chindapusa cha ndalama zokwana madola 12,000 a ku America, chifukwa chopezeka pamsonkhano wachipembedzo wosavomerezedwa ndi boma.Chaposachedwapa, pa January 11 ndi March 2, 2014, apolisiwo anachitanso zinthu zina zosokoneza misonkhano ya Mboni za Yehova.

  • Kuunika Chilichonse Chimene Chili M’mabuku a Mboni

    Pa mayiko onse amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya, ndi dziko la Azerbaijan lokha a lomwe limaunika mabuku onse achipembedzo asanalowe kapena kufalitsidwa m’dzikoli. Koma zimenezi n’zosemphana ndi malamulo a dzikoli. b Boma la Azerbaijan limaletsa kapena kuchepetsa chiwerengero cha mabuku othandiza pophunzira Baibulo amene a Mboni za Yehova amaitanitsa kuchokera kumayiko ena a m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya. Pa mabuku amene boma linaletsa, pali magazini osiyanasiyana a Nsanja ya Olonda, omwe amatuluka kawiri pamwezi. c Makhoti a m’dzikoli akukana kuthandiza a Mboni pa madandaulo awo okhudzana ndi zimene boma likuchita poletsa mabuku awo.

Zimene Mabungwe a M’mayiko ena Akunena pa Nkhani ya Zimene Boma la Azerbaijan Likuchita Posalemekeza Ufulu Wopembedza

Mabungwe ambiri oona za ufulu wachibadwidwe a m’mayiko osiyanasiyana, afufuza ndiponso anenapo maganizo awo pa nkhani ya malamulo a dziko la Azerbaijan okhudzana ndi chipembedzo komanso mmene bomalo likuchitira zinthu ndi magulu osiyanasiyana azipembedzo.

  • Lipoti lapachaka la mu 2013, lomwe linatulutsidwa ndi bungwe lina la ku America loona za ufulu wa zipembedzo, linati: “Ngakhale kuti boma la Azerbaijan likunena kuti anthu a m’dzikolo ali ndi ufulu wopembedza, bomalo likuchitira nkhanza magulu ena azipembedzo, makamaka chifukwa cha lamulo lopondereza zipembedzo limene linakhazikitsidwa m’chaka cha 2009.”

  • Lipoti limene bungwe lina la ku Ulaya lolimbana ndi tsankho linatulutsa, linasonyeza kuti bungweli ndi lokhudzidwa kwambiri ndi mmene boma la Azerbaijan likuponderezera magulu azipembedzo zosiyanasiyana. Pofotokoza za malamulo a boma la Azerbaijan okhudza zipembedzo, bungweli linati: “Tikufunitsitsa kuti boma la Azerbaijan lisinthe malamulo ake kuti agwirizane ndi mfundo zimene mayiko a ku Ulaya anagwirizana m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.”

  • Komiti yoona za malamulo ya Bungwe la Mayiko a ku Ulaya, yomwe imachita misonkhano yake ku Venice, inalemba chikalata chomveka bwino chouza boma la Azerbaijan kuti lisinthe malamulo ake kuti lizilemekeza ufulu umene anthu ali nawo pa nkhani yolambira. M’chikalatacho, komitiyi inati: “Boma la Azerbaijan lili ndi malamulo ambiri opondereza omwe ndi osagwirizana ndi malamulo amene mayiko amafunika kumayendera. . . . Bomali liyenera kusintha malamulo ake okhudza ufulu wopembedza ndiponso ufulu woti munthu azichita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira. Liyeneranso kusintha malamulo okhudza kulembetsa zipembedzo. Ndipo lisamalowerere m’zochita za zipembedzo ngakhalenso kuthetsa magulu a zipembedzo. Bomali likuyenera kukonzanso malamulo ake okhudzana ndi nkhani yokana kulowa usilikali ndiponso ufulu wa zipembedzo wouza ena zikhulupiriro zawo. Kuwonjezera pamenepa, bomali liyenera kusintha malamulo ake okhudza kufalitsa ndi kugawa mabuku achipembedzo.”

A Mboni Amaona Kuti Ufulu Wosiyanasiyana ndi Wofunika Kwambiri

A Mboni za Yehova padziko lonse amaona kuti ufulu wosiyanasiyana, monga wolankhula za kukhosi, wosonkhana pamodzi, wochita zimene munthu amakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza, ndi wofunika kwambiri. Iwo amasangalala ngati boma likulemekeza ufulu umenewu. Gulu lochepa la anthu 2,500 a Mboni za Yehova komanso anthu ena amene amalambira nawo Mulungu m’dziko la Azerbaijan, akuyembekeza kuti bomalo liyamba kulemekeza ufulu wawo wolambira Mulungu ngati mmene likulemekezera ufulu wa zipembedzo zina za m’dzikoli.

a Dziko la Azerbaijan linalowa m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya pa January 25, 2001.

b Gawo 48 la malamulo a dzikoli limapereka ufulu wolambira, ndipo gawo 50 limaletsa kuunika mabuku kapena nkhani zimene zimafalitsa m’dzikoli.

c Mwezi uliwonse, a Mboni za Yehova amafalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda imene amagawira anthu ena ndipo imafotokoza zimene Baibulo limaphunzitsa. Palinso magazini ina ya Nsanja ya Olonda imene imafalitsidwa mwezi uliwonse, yomwe amaigwiritsa ntchito pophunzira Baibulo m’mipingo yawo. Magazini a Nsanja ya Olonda amafalitsidwa kwambiri kuposa magazini ena aliwonse padziko lonse. Izi zili choncho chifukwa magazini okwana 45,000,000 amafalitsidwa mwezi uliwonse m’zinenero zoposa 200.