3 JUNE, 2022
BENIN
Buku la Mateyu Latulutsidwa M’Chifoni
Pa 29 May 2022, M’bale Sylvain Bois wa m’Komiti ya Nthambi ya Benin anatulutsa Baibulo la Uthenga Wabwino wa Mateyu mu chilankhulo cha Chifoni. Buku la m’Baibuloli logwiritsa ntchito pazipangizo zamakono linatulutsidwa pa msonkhano wochita kujambulidwa. Ofalitsa pafupifupi 7,000 komanso anthu achidwi anamvetsera pulogalamu yamsonkhanowu. Baibulo lochita kusindikizidwa lidzayamba kupezeka mu December, 2023.
Ngakhale kuti panali kale Mabaibulo ena mu Chifoni Baibuloli lisanatulutsidwe, mu Mabaibulowa anachotsamo dzina la Mulungu komanso muli mawu ambiri omwe safotokoza molondola mawu a m’Baibulo loyambirira. Chinanso ndi chakuti, Mabaibulowa ndi okwera mtengo, komanso ochita malonda amakana kugulitsa a Mboni za Yehova.
Baibulo latsopanoli la uthenga wabwino wa Mateyu linamasuliridwa molondola mogwirizana ndi uthenga womwe unali m’Baibulo la m’chilankhulo choyambirira. Mwachitsanzo, pa Mateyu 10:28 pamanena kuti: “Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo.” Mawu am’munsi a pavesili amasonyeza kuti mawu a m’Baibulo loyambirira omwe anawamasulira kuti “moyo,” amatanthauza “chiyembekezo chodzakhala ndi moyo.” Zinthuzi zidzathandiza ofalitsa akamaphunzitsa anthu achidwi mu utumiki.
M’bale Palle Bjerre wa m’Komiti ya Nthambi ya Benin ananena kuti: “Tili ndi mabuku ambiri ofotokozera mawu a m’buku la Mateyu. Choncho kukhala ndi buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu lomasuliridwa bwino zitithandiza tikamaphunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino. Tikuyamikira kwambiri Yehova komanso abale ndi alongo omasulira chifukwa cha khama lomwe anasonyeza kuti buku la m’Baibuloli lipezeke.”
Tili ndi chikhulupiriro kuti Baibuloli lithandiza abale ndi alongo olankhula Chifoni kupitirizabe kuyandikira Yehova komanso kuthandiza ena kuti apitirize kutero.—Mateyu 5:3.