Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 3, 2019
BOLIVIA

Nthaka Yogumuka Inaononga Zinthu M’dera la La Paz M’dziko la Bolivia

Nthaka Yogumuka Inaononga Zinthu M’dera la La Paz M’dziko la Bolivia

Pa 30 April, 2019, nthaka yomwe inagumuka inaononga chigawo chachikulu cha dera la San Jorge Kantutani mumzinda wa La Paz ku Bolivia. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambirimbiri athawe m’nyumba zawo.

Ngakhale kuti palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa kapena kuvulala, ofesi ya nthambi ya ku Bolivia yanena kuti nyumba ziwiri za abale athu zinaonongekeratu chifukwa cha kugumuka kwa nthakako. Komanso, pali mabanja ena 11 a a Mboni omwe amakhala m’dera lomwe lakhudzidwa ndi ngoziyi amene nyumba zawo zinaonongeka pang’ono koma zina sizinaonongeke.

Mogwirizana ndi malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi, abale a m’Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi, oyang’anira madera, komanso akulu a m’mipingo akulimbikitsa abale ndi alongo okhudzidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba komanso kuwapatsa zinthu zofunikira. Abale onse amene akukhala m’madera omwe akhudzidwa ndi ngoziyi akukhala mwatcheru chifukwa pali chiopsezo choti nthaka ikhoza kugumukanso ngati mvula ingapitirize kugwa.

Tikusangalala kuti abale athu sanavulale komanso kuti akupatsidwa zinthu zofunika pamoyo.—Agalatiya 6:10.