Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 29, 2019
BRAZIL

A Mboni za Yehova Anaonetsa Mabuku a pa JW.ORG Othandiza Anthu a Vuto Losamva ndi Osaona Pachionetsero cha Mabuku ku Rio

A Mboni za Yehova Anaonetsa Mabuku a pa JW.ORG Othandiza Anthu a Vuto Losamva ndi Osaona Pachionetsero cha Mabuku ku Rio

A Mboni za Yehova anakhala nawo pa Chionetsero cha Nambala 19 Chapadziko Lonse cha Mabuku cha ku Rio de Janeiro, chimene chinachitikira ku Riocentro Convention and Event Center kuyambira pa 30 August mpaka pa 8 September, 2019. Pachionetserochi, chimene ndi chionetsero chachikulu kwambiri chazachikhalidwe ku Brazil, panaikidwa malo okwana 520 oonetsera zinthu ndipo panabwera alendo okwana pafupifupi 600,000. Abale athu nawonso anali ndi malo awo pachionetserochi ndipo ankasonyezapo webusaiti yathu komanso ntchito imene timagwira yothandiza anthu kupindula ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Pa masiku 10 amene chionetserochi chinachitika, abale ndi alongo okwana 258 amene anadzipereka kuthandizapo anagawira mabuku okwana 3,737.

Pamalo athu oonetsera panali mbali yapadera yokhala ndi mabuku othandiza anthu a vuto losamva, ovutika kumva, komanso osaona. Abale anaonetsa mavidiyo a m’chinenero chamanja cha ku Brazil, ndipo panali ofalitsa amene amachidziwa bwino chinenerochi kuti azithandiza alendo. Mmodzi mwa ofalitsa ongodzipereka amene anali pamalopo anati: “Munthu akafika pamalo oonetserawo, amamasuka kulankhula nafe ndipo samachita manyazi. Nthawi zonse pamakhala munthu woti afotokoze mmene webusaiti ya jw.org imagwirira ntchito komanso zimene zimachitika pa phunziro la Baibulo.”

Wofalitsa wavuto losaona wazaka 10 akufotokozera mtolankhani momwe mabuku a anthu avuto losaona a Mboni za Yehova amuthandizira

Mphunzitsi wina anafika pamalo oonetserawo ndi ana asukulu 7 a vuto losamva. Iye anachita chidwi kwambiri ndi mabuku a pa jw.org a m’chinenero chamanja othandiza achinyamata. Iye anati nthawi zambiri makolo amamupempha kuti awathandize kufotokozera ana awo a vuto losamva nkhani zoumitsa pakamwa. Mphunzitsiyo anati tsopano iye aziuza makolowo kuti angopita pawebusaiti yathu.

Mmodzi mwa alongo athu akuonetsa mlendo mabuku ofotokoza za m’Baibulo

Pamalo oonetserawo panalinso masikilini oti munthu akhoza kudinapo omwe anamasuliridwa m’zinenero za anthu ochokera m’midzi ya ku Brazil zomwe zikupezeka pa jw.org, monga Chigwarani, Chitsikuna, ndi Chisavanti. Ricardo Carneiro, amene ankaimirira a Mboni za Yehova pamalopo, anati: “Cholinga chathu n’choti tithandize anthu ochokera m’midzi ya ku Brazil kuno kuti azitha kulimvetsa Baibulo m’chinenero chawo.”

Chionetsero Chapadziko Lonse cha ku Rio chimenechi chimalimbikitsa anthu kuwerenga, n’cholinga chopititsa patsogolo miyoyo ya anthu a ku Brazil. Alendo masauzande ambiri amene anapita pamalo oonetsera a jw.org anapatsidwa mwayi wowerenga Baibulo ndi mabuku ena m’chinenero chawo. Kuwerenga zinthu zimenezi kwathandiza anthu kwa zaka zambiri kupititsa patsogolo miyoyo yawo.—2 Timoteyo 3:16, 17.