Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 12, 2019
BRAZIL

Damu Lagumuka N’kupha Anthu ku Brazil

Damu Lagumuka N’kupha Anthu ku Brazil

Lachisanu pa 25 January, 2019, damu la pa mgodi wina mumzinda wa Brumadinho womwe uli m’chigawo cha Minas Gerais ku Brazil, linagumuka zomwe zinachititsa kuti matope akokoloke n’kupha anthu. Anthu osachepera 150 anafa, ndipo enanso 182 akusowa.

Mumzinda wa Brumadinho muli mipingo iwiri yomwe ili ndi a Mboni pafupifupi 180, ndipo ambiri mwa a Mboniwo amagwira ntchito pakampani ya zamigodi. Pa nthawi yomwe damulo linkagumuka, abale 10 anali akugwira ntchito pamalopo. Abale 9 sanavulale koma n’zomvetsa chisoni kuti m’bale mmodzi yemwe amatumikira monga mkulu sakupezeka. Kuonjezera pamenepo, mabanja a Mboni osachepera 5 anathawa m’nyumba zawo ndipo nyumba imodzi inawonongekeratu.

M’bale mmodzi wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Brazil komanso oyang’anira madera a m’chigawocho, anayendera anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi kuti akawalimbikitse ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwapatsa zinthu zofunikira. Tikupemphera kuti Atate wathu wakumwamba apitirize kutonthoza ndi kulimbikitsa onse omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.—Aroma 15:5.