4 JANUARY, 2022
BRAZIL
Mvula Yamkuntho Yachititsa Madzi Kusefukira Kumpoto Chakum’mawa kwa Dziko la Brazil
Kuyambira pa 24 mpaka 26 December 2021, mvula yamphamvu inagwa ku Bahia State, m’dziko la Brazil ndipo anthu oposa 640,000 anakhudzidwa ndi mvulayi. Madzi osefukirawa anagumula madamu ndipo izi zinachititsa kuti mizinda yambiri isefukire komanso kuti anthu azunguliridwe ndi madzi n’kusowa kolowera.
Mmene Zinakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Palibe aliyense amene anavulala
Ofalitsa 273 anakakamizika kusamuka m’nyumba zawo
Nyumba zokwana 109, zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Panakonzedwa Komiti Yothandiza Pangozi Zamwadzidzidzi kuti ipereke madzi, chakudya ndi zovala kwa anthu okhudzidwa
Ofalitsa omwe anasamuka m’nyumba zawo, akusungidwa ndi achibale awo komanso ofalitsa ena mongoyembekezera
Ntchito yopereka chithandizoyi ikugwiridwa motsatira njira zonse zodzitetezera ku COVID-19
M’bale Marcelo Ambrósio amene ali m’Komiti Yothandiza Pangozi Zamwadzidzidzi ananena kuti: “Kuona chikondi chimene abale ndi alongo anasonyezana pa nthawi yangoziyi, kwatilimbikitsa kuti tizitumikirabe Yehova mwakhama.”
Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kukhala “malo okwezeka ndiponso achitetezo” kwa abale athu omwe anakhudzidwa ndi mvula yamkunthoyi—Salimo 9:9.