Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 10, 2019
BRAZIL

Ntchito Yapadera Yolalikira Inathandiza Anthu M’madera a Kumidzi ku Brazil

Ntchito Yapadera Yolalikira Inathandiza Anthu M’madera a Kumidzi ku Brazil

A Mboni za Yehova masauzande ambirimbiri akuyesetsa kuchita khama kuti alalikire uthenga wa m’Baibulo kwa anthu omwe amakhala m’madera a kumidzi ku Brazil. Ntchito yapadera yolalikirayi inayamba pa 1 September, 2018, ndipo inatha pa 31 December, 2019. Pofika pano, ofalitsa oposa 80,000 agwira nawo ntchitoyi ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo oposa 16,000.

Dziko la Brazil ndi la nambala 5 pa mayiko aakulu kwambiri padziko lonse. Zikuoneka kuti m’dzikoli anthu pafupifupi 28 miliyoni amakhala m’madera a kumidzi. Anthu enanso 22 miliyoni amakhala m’matawuni ndi m’midzi yomwe ili kutali kwambiri. Panopa ofalitsawa alalikira kale m’magawo oposa 1,600. Ofalitsa ena anafunika kuyenda mtunda wa makilomita oposa 2,000 kuti akafike komwe kuli anthu.

Wofalitsa wina anafika pakhomo la bambo wina wachikulire ndipo anamupeza akusenda khofi yemwe anakolola. Bamboyu anauza wofalitsayo kuti alowe m’nyumba kenako anaitana mkazi wake n’kumuuza kuti: “Anthuwa abwera kudzatiuza zokhudza Baibulo. Bwerani timvetsere!”

Bamboyu ndi mkazi wake anayamba kufunsa mafunso. Iwo ankafuna kudziwa zimene zimachitika munthu akamwalira, chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika, mmene anthu okwatirana angathetsere mavuto a m’banja, komanso ngati n’zoyenera kumapereka chakhumi ndi nkhani zinanso zambiri. Chifukwa chosangalala ndi mmene wofalitsayu anayankhira mafunsowa pogwiritsa ntchito Baibulo, bamboyu anafotokoza kuti m’mawa wa tsikuli amapemphera kwa Mulungu ngati mafunso ake ambirimbiriwa angayankhidwe. Kenako madzulo ake banjali linapita kumisonkhano koyamba ndipo likupitirizabe kuphunzira Baibulo.

M’gawo lina, ofalitsa ena ankalalikira nyumba ndi nyumba ndipo mvula yamphamvu inayamba kugwa zomwe zinachititsa kuti athawire pachipatala chinachake. Ali m’chipatalacho, anafunsa mayi wina ndi mwana wake kuti anene zimene angakonde kufunsa Mulungu. Mwana wa mayiyo ananena kuti angakonde kudzaonananso ndi agogo ake aakazi omwe anamwalira. Ofalitsawa anawawerengera malemba okhudza kuuka kwa akufa komanso anasonyeza vidiyo yamutu wakuti Posachedwapa Tidzakumananso ndi Amene Anamwalira.

Pa nthawi ina, ofalitsawa atapita kunyumba ya mayiyu anayamba kuphunzira naye Baibulo limodzi ndi banja lake. Mayiyu ndi ana ake aakazi anapita kumisonkhano m’tawuni ina yapafupi ndipo akupitiriza kuphunzira kudzera pafoni.

Baibulo linalosera kuti nzika za Ufumu wa Mulungu zidzafika “kumalekezero a dziko lapansi.” Ntchito yapadera yolalikira yomwe inachitika m’madera a kumidzi ku Brazil, ndi umboni wosonyeza kuti chifuniro cha Yehova chikuchitika pokwaniritsa ulosiwu.—Salimo 72:8.