FEBRUARY 4, 2020
BRAZIL
Ntchito Yokonza Zinthu Zomwe Zinawonongeka ndi Madzi Osefukira ku Brazil
Kungoyambira pa 18 January 2020, mvula yamphamvu kwambiri yakhala ikugwa m’madera a Espírito Santo ndi Minas Gerais ku Brazil. Zimenezi zinachititsa kuti madzi asefukire n’kuwononga zinthu zambiri. Madzi osefukirawa anagwetsa nyumba, kukokolola magalimoto komanso kugwetsa mitengo. Malipoti akusonyeza kuti anthu masauzande anathawa m’nyumba zawo ndipo anthu oposa 60 anafa.
Ku Espírito Santo
M’matawuni a Iconha ndiponso Alfredo Chaves, madziwa anawononga nyumba 9 zomwe munkakhala abale ndi alongo athu 27. Mwamwayi, palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene anavulala kapena kufa.
A Mboni ena 100 a m’derali anadzipereka kugwira ntchito yothandiza abale omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukirawa. Akulu a m’mipingo anayendetsa dongosolo logawa zinthu zimene abale anapereka monga chakudya, madzi ndi zovala. Anathandizanso pa ntchito yoyeretsa komanso kuchotsa matope m’nyumba za abale ngakhalenso za anthu ena omwe si Mboni.
Ku Minas Gerais
Palibe m’bale kapena mlongo yemwe anavulala kapena kufa. Komabe, Nyumba za Ufumu 5 zinawonongeka ndiponso mabanja 50 a Mboni anathawa m’nyumba zawo. Abale ena anatsakamira mu nsanjika yachiwiri ya nyumba zomwe amakhala chifukwa cha kuchuluka kwa madzi osefukirawa moti anapulumuka anthu atakawatengako pa boti. Abale ndi alongo onse omwe anathawa m’nyumba zawo anakakhala nawo m’nyumba za a Mboni za Yehova anzawo.
Makomiti opereka chithandizo pakagwa mavuto amwadzidzidzi anakhazikitsidwa ku Espírito Santo ndi ku Minas Gerais kuti ayendetse ntchito yothandiza anthu. Makomitiwa akugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera ndiponso akulu a m’maderawa poonetsetsa kuti abale ndi alongo omwe akuvutika chifukwa cha madzi osefukirawa, alandira chithandizo komanso kulimbikitsidwa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.
Tipitirizabe kupempherera abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi madzi osefukirawa. Tikuthokoza Yehova chifukwa chowapatsa mphamvu, kuwatonthoza komanso kuwapatsa thandizo kudzera m’gulu lathu lachikhristu.—Salimo 28:7.