Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 18, 2019
BRAZIL

Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku São Paulo, Brazil

Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku São Paulo, Brazil
  • Masiku: 12 mpaka 14 July, 2019

  • Malo: São Paulo Expo ku São Paulo, Brazil

  • Zinenero: Chinenero Chamanja cha ku Brazil, Chingelezi, Chifulenchi, Chitaliyana, Chipwitikizi, Chisipanishi

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 36,624

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 291

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 7,000

  • Nthambi Zoitanidwa: Angola, Argentina, Belgium, Czech-Slovak, France, Italy, Mozambique, Portugal, Scandinavia, Suriname, Trinidad ndi Tobago, United States, Venezuela

  • Zina Zomwe Zinachitika: Mayi Maria Luiza Gonçalves omwe ndi woyang’anira za mauthenga ku malo oonetserako zinyama a São Paulo Zoo, analandira alendo ochokera ku mayiko ena ndipo anati: “Timakhala ndi zochitika zosiyanasiyana ku malo ano. Timalandira alendo ambiri chaka chonse, koma sindinaonepo gulu lalikulu chonchi la anthu aubwenzi komanso ochita zinthu mwadongosolo. Ndinu anthu okondana kwambiri. Tikuona mmene mumasonyezerana chikondi mukamahagana, mukamachitirana zinthu mokoma mtima komanso mukamaimba nyimbo.”

 

Abale ndi alongo a ku Brazil akulandira alendo pa bwalo la ndege la São Paulo Guarulhos International Airport

Abale 4 a ku São Paulo ndi ku ofesi ya nthambi ya ku Brazil akuchita msonkhano ndi atolankhani pofuna kudziwitsa anthu za msonkhano wamayikowu

Alendo ochokera ku mayiko ena akulalikira limodzi ndi abale a ku São Paulo

Alendo ochokera ku mayiko ena ali panja pa malo a msonkhano pa tsiku loyamba la msonkhanowu

Abale ndi alongo akulemba manotsi pamene akumvetsera msonkhanowu

Lachisanu, M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza

Abale akubatiza anthu Loweruka masana

Alongo akumasulira nkhani m’Chinenero cha Manja chochita kugwirana ndi anthu omwe ali ndi vuto losamva komanso losaona omwe ali pamsonkhanowu

Alendo akujambulitsa panja pa malo a msonkhanowu

Abale ndi alongo omwe ali mu utumiki wanthawi zonse wapadera akubayibitsa anthu Lamlungu, pambuyo pa msonkhanowu