DECEMBER 31, 2018
BRAZIL
Moto Wolusa Wawononga ku Manaus M’dziko la Brazil
M’mawa kwambiri pa 18 December, moto unayaka mumzinda wa Manaus ku Brazil, ndipo unawononga nyumba zosachepera 600. Ngakhale kuti palibe amene anafa ndi motowu, anthu 4 anavulala ndipo enanso 2,000 anathawa m’nyumba zawo.
Ofesi ya nthambi ku Brazil yanena kuti palibe m’bale kapena mlongo amene anafa kapena kuvulala ndi motowu. Komabe, nyumba 10 za abale athu zinawonongeka ndipo zimenezi zinachititsa kuti ofalitsa 18 komanso achibale awo omwe si Mboni athawe m’nyumba zawo. Motsogoleredwa ndi ofesi ya nthambi, Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi ikuthandiza ofalitsa amene akhudzidwa ndi motowu.
Tili ndi chikhulupiriro kuti abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi moto ku Brazil apitiriza kudalira Yehova yemwe ndi ‘malo athu okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso.’—Salimo 9:9, 10.