Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 8, 2020
BULGARIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lapereka Chigamulo Chokomera a Mboni za Yehova ku Bulgaria

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lapereka Chigamulo Chokomera a Mboni za Yehova ku Bulgaria

Pa 10 November 2020, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linagamula kuti boma la Bulgaria linaphwanya ufulu wolambira wa abale athu. Zimenezi zikutanthauza kuti ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu mumzinda wa Varna ku Burgaria ikuyenera kupitirira. Abale athu akhala akulephera kumaliza kumanga Nyumba ya Ufumuyi chifukwa kwa zaka zopitirira 10 akhala akutsutsidwa ndi akuluakulu a boma. Choncho Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linalamula boma la Bulgaria kuti lipatse abale athu chipepeso cha ndalama zokwana madola 11,500 a ku America.

Mlandu wake unali wokhudza kumangidwa kwa Nyumba ya Ufumu pamalo amene abale athu anagula mu January 2006. Mu May 2007 akuluakulu a boma ku Varna anapatsa abale athu chilolezo choti amange Nyumba ya Ufumu ndipo anayambadi kumanga. Koma mu July chaka chomwecho meya wa mzinda wa Varna ananena kuti abalewo sakumanga bwino Nyumba ya Ufumu ndipo anawauza kuti asiye kumangako. M’mwezi womwewu, a chipani china chodziwika bwino ku Bulgaria anakaika zikwangwani pamalo omwe amamangapo Nyumba ya Ufumu paja kenako anamema anthu ambirimbiri n’kupanga zionetsero posonyeza kuti sakugwirizana ndi zoti Nyumba ya Ufumuyi imangidwe.

Malinga ndi chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe, akuluakulu a boma ku Varna anasonyeza poyera kuti akufuna kuipitsa a Mboni za Yehova ndipo iwowo ndi amene “anachititsa kuti anthu apange zionetserozo.” Nayenso meya wa mumzindawu anachita kunena m’nyumba zofalitsa nkhani kuti akugwirizana ndi zionetserozi.

Ngakhale kuti anachita kusonyezeratu kuti akudana ndi a Mboni za Yehova, meya wa mzindawu ndi akuluakulu ena ananena kuti analetsa ntchito yomangayo chifukwa chakuti panali kusamvana pa nkhani malamulo okhudza malire osati chifukwa chodana ndi chipembedzo cha Mboni za Yehova.

Abale athu anapanga apilo za nkhaniyi kumakhoti a ku Bulgaria maulendo ambirimbiri komanso anakapanga apilo ku Khoti Lalikulu Kwambiri m’dzikoli koma sanaloledwe kuti apitirize kumangako. Zimenezi zinachititsa kuti nthawi ina mpingo wa m’derali upange lendi malo ochitiramo misonkhano.

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linanena kuti zimene akuluakuluwa anachita n’zosemphana ndi malamulo. Oweruza 6 pa oweruza 7 a khotili anagwirizana ndi zoti kuletsa ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu komwe akuluakulu a boma ku Varna anachita ndi kuphwanya “ufulu wa maganizo, chikumbumtima komanso wopembedza” mogwirizana ndi Gawo 9 ndi 11 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe.

Abale athu ali ndi chikhulupiriro choti akuluakulu a mzindawu panopa ayamba kugwiritsa ntchito chigamulo cha khotili ndipo awapatsa chilolezo chopitiriza kumanga malo olambirira. Malowa athandiza anthu m’derali komanso alemekeza dzina la Yehova mumzinda wa Varna. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chotithandiza nthawi zonse.—Salimo 54:4.