Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

BULGARIA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Bulgaria

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Bulgaria

A Mboni za Yehova anayamba kupezeka ku Bulgaria kuyambira mu 1888. Ndipo mu 1938 iwo analembetsa ku boma kuti akhale chipembedzo chovomerezeka, koma dzikolo litakhala la chikomyunizimu mu 1944, chipembedzo cha Mboni za Yehova sichinalinso chovomerezeka. Kuyambira pa nthawiyi a Mboni ankaletsedwa kuchita zinthu zokhudza kulambira mpaka mu 1991 pamene bungwe lawo la Christian Association of Jehovah’s Witnesses, linalembetsedwanso. Komabe, pofika mu 1994, a Mboni za Yehova ndi zipembedzo zinanso zing’onozing’ono anakhalanso osavomerezeka. Zimenezi zinachitika pambuyo pa kampeni yoipitsa mbiri ya zipembedzo zomwe sizinkachita zinthu zokhudza chikhalidwe, komanso kukhazikitsidwa kwa malamulo okhwima okhudza zipembedzo. Kenako apolisi anayamba kumanga a Mboni, kusokoneza misonkhano yawo, komanso kulanda mabuku awo. Makhoti a m’dzikolo sanathandize a Mboniwo.

Popeza kuti makhoti a m’dzikolo sanawathandize a Mboniwo, iwo anakadandaula za nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. M’chaka cha 1998, 2001, komanso mu 2004 khotili linagwirizana ndi zomwe a Mboni anakambirana ndi boma la Bulgaria. Pambuyo pa zokambiranazi, boma linavomereza kuti a Mboni za Yehova alembetsenso chipembedzo chawo. Khotili linapatsanso a Mboni maufulu osiyanasiyana okhudza kupembedza monga ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, ufulu wosankha kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali komanso ufulu wofotokozera ena zimene amakhulupirira popanda kusokonezedwa.

A Mboni za Yehova ku Bulgaria akuyamikira kuti aliko ndi ufulu wochepa wopembedza ndipo amatha kuchita zinthu zokhudza kulambira popanda chosokoneza. Komabe, akuluakulu ena oyang’anira mizinda amagwiritsa ntchito molakwika malamulo omwe anawakhazikitsa m’madera poletsa a Mboni za Yehova kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri komanso amakana kupereka chilolezo choti a Mboni apeze malo omangapo Nyumba za Ufumu zawo. Komanso anthu ena anamenya ndi kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova. Ngakhale kuti akuluakulu azamalamulo amathandiza a Mboni, nthawi zambiri iwo samanga anthu amene amachita za nkhanzazi kapena kuteteza anthu amene achitidwa nkhanza. A Mboni akupitiriza kukambirana ndi akuluakulu a boma la Bulgaria n’cholinga chofuna kuthetsa nkhanizi, komanso nkhani yokhudza kupatsidwa malo omangapo Nyumba ya Ufumu ili ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe.