Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 26, 2018
CAMEROON

Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Cameroon Ili Mkati

Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Cameroon Ili Mkati

Mumzinda wa Douala ku Cameroon, muli atumiki anthawi zonse a pa Beteli okwana 50. Panopa akugwiritsa ntchito maofesi amene ali m’dera la Bonabéri mumzindawu, koma posachedwapa ayamba kugwiritsa ntchito maofesi atsopano omwe akumangidwa m’dera la Logbessou. Kumangidwa kwa ofesi ya nthambi yatsopanoyi kukusonyeza kuti chiwerengero cha ofalitsa chikuwonjezereka m’dzikoli. M’chaka cha 2017, chiwerengero cha anthu omwe anapezeka pa mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu ku Cameroon chinali choposa 100,000, kuwirikiza kawiri chiwerengero cha ofalitsa a m’dzikoli.

Abale athu akuika mawaya oteteza ku mphezi.

Ofesiyi ikumangidwa pamalo amene pali kale Nyumba ya Msonkhano ndipo ntchitoyi yayamba ndi kukumba maziko. Ntchito yomangayi ikadzatha, ofesiyi idzaoneka ngati mmene nyumba zambiri za m’derali zimamangidwira ndipo maofesi adzakhala paokha, ngati mmene chithunzi chili pamwambapa chikusonyezera. Pali chiyembekezo choti banja la Beteli lisamukira ku nthambi yatsopanoyi chakumapeto kwa chaka cha 2019.

A Gilles Mba, omwe ndi a m’banja la Beteli ku Cameroon ndipo akutumikira mu Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani anati, “N’zosangalatsa kuona kuti abale ndi alongo athu ambirimbiri asonyeza mzimu wa Yesaya ndipo adzipereka kuti agwire nawo ntchito yomangayi.” (Yesaya 6:8) Iwo ananenanso kuti, “Ntchito yosangalatsayi yatilimbikitsa kwambiri tonse amene tikutumikira panthambi pano. Ndife okonzeka kuyamba kugwiritsa ntchito maofesi atsopanowa pofuna kukwaniritsa cholinga chake chomwe ndi kulemekeza dzina la Yehova.”

Ena mwa abale ndi alongo oposa 2,800 omwe anapezeka pamsonkhano wophunzira mmene angathandizire pantchito yomanga nthambi yatsopano.