Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale ndi Mlongo Mudaheranwa omwenso akuchita upainiya, akupita kuntchito

APRIL 6, 2020
CANADA

Kupeza Mtendere pa Nthawi Yovuta

Kupeza Mtendere pa Nthawi Yovuta

M’bale Jean-Yves komanso mkazi wake, Vasthie Mudaheranwa akugwira ntchito yothandiza anthu omwe akudwala matenda a kolonavailasi mumzinda wa Montreal ku Canada. M’bale Mudaheranwa ndi dokotala ndipo Mlongo Mudaheranwa ndi nesi pachipatala chothandiza anthu omwe akudwala matenda a COVID-19. Pomwe anthu ochuluka akuda nkhawa kwambiri, M’bale ndi Mlongo Mudaheranwa akudalira Yehova kuti awapatsa mphamvu ndiponso “chimwemwe mumtima” mogwirizana ndi mmene analonjezera.​—Yesaya 65:14.

M’bale Mudaheranwa anati: “Azinzanga ambiri ogwira nawo ntchito ali ndi mantha kwambiri ndipo sindinawaonepo ali ndi mantha chonchi.” Mlongo Mudaheranwa anati: “Kuphunzira Baibulo pawekha kumathandiza kwambiri. Tikumaganizira zoti chimenechi ndi chizindikiro cha masiku otsiriza ndipo tikumadzikumbutsa kuti Yehova ali nafe ndipo sangatisiye. Tikumapempheranso kwa Yehova ndipo zimenezi zikumatithandiza kwambiri. Ndikumapemphera ndisanapite kuntchito komanso ndisanayambe ntchito ndipo kuchita zimenezi kwandithandiza kuti ndizipeza mtendere.”

M’bale ndi Mlongo Mudaheranwa ali pamisonkhano yampingo

M’bale Mudaheranwa anati: “Ndinachokera ku Rwanda ndipo ndinapulumuka pa nthawi imene m’dzikoli munali nkhondo yoopsa yomwe anthu ankaphana chifukwa chosiyana mitundu. Ku Canada kuno sitinakumanepo ndi zimenezi, choncho nthawi zina tikhoza kuiwala kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Ndivomereze kuti nanenso sindinkaganizira zoti tsiku la Yehova lili pafupi kwambiri. Matenda oopsawa andichititsa kutsimikizira kwambiri kuti tikukhala m’masiku otsiriza ndipo zimenezi zandilimbikitsa kuti ndizikhulupirira kwambiri Baibulo ndi maulosi a m’Baibulo.”

Nawonso anthu a Yehova padziko lonse ali ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha M’bale ndi Mlongo Mudaheranwa pamene akupitiriza kupeza mtendere pa nthawi yovuta kwambiri imeneyi.​—Yesaya 48:18.