MAY 17, 2019
CANADA
Madzi Asefukira Kwambiri ku Canada
Anthu masauzande ambiri omwe amakhala m’zigawo za New Brunswick, Ontario, ndi Quebec m’dziko la Canada, anasamuka m’nyumba zawo chifukwa cha madzi osefukira. M’chigawo cha Quebec chokha, anthu 9,000 anasamutsidwa m’nyumba zawo.
Ofesi ya nthambi ku Canada yanena kuti nyumba 44 za abale athu ku Quebec zinaonongeka. Panopa sitinalandire lipoti lililonse lochokera ku New Brunswick ndi ku Ontario losonyeza kuti madziwa aononga zinthu koma madzi akupitirizabe kusefukira.
Oyang’anira madera limodzi ndi akulu a mipingo ya m’madera omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukirawa ku Quebec, akulimbikitsa ofalitsa omwe anakhudzidwa. Komanso m’bale wochokera ku ofesi ya nthambi anapita kukalimbikitsa mwauzimu abale ndi alongo kumadera amene madzi osefukirawa anaononga kwambiri. M’chigawo cha Beauce, abale ndi alongo amaliza kale mbali yoyamba ya ntchito yoyeretsa komanso kuchotsa matope m’nyumba 20 za abale athu zomwe munalowa madzi osefukirawa. Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi inakhazikitsidwa kuti ithandize anthu omwe nyumba zawo zinaonongeka ku Sainte-Marthe-sur-le-Lac.
Tikupemphera kuti abale ndi alongo athu amene akhudzidwa ndi madzi osefukira posachedwapa, apitirize kudalira Yehova yemwe ndi ‘mphamvu ndi nyonga yawo.’—Ekisodo 15:2.