26 DECEMBER 2023
CHILE
A Mboni Analalikira Uthenga Wabwino Kumpikisano wa Masewera a Mayiko a ku America M’dziko la Chile
Mpikisano wa Masewera a Mayiko a ku America wa 2023 unachitika m’mizinda yosiyanasiyana ku Chile, kuyambira pa 20 October mpaka pa 5 November 2023. Akatswiri oposa 6,900 a masewera osiyanasiyana ochokera m’mayiko 46, anachita nawo mpikisanowu. A Mboni za Yehova pafupifupi 1,500 anagwira ntchito yapadera yolalikira pa nthawi ya masewerawa. M’mizindayi munaikidwa mashelefu amatayala okhala ndi mabuku a Chingelezi, Chipwitikizi ndi Chisipanishi. Abale athu anasangalala kwambiri kucheza ndi akatswiri ochita masewerawa komanso odzaonerera.
Pa nthawi ina, katswiri wina wotchuka anabwera pamene abale anaima ndi kashelefu. Iye anawafotokozera kuti ali mnyamata, ankapita kumisonkhano ndi mayi ake. Ngakhale kuti panopa ntchito yakeyi imamuthandiza kupeza ndalama zambiri, zimenezi sizinamuthandize kukhala wosangalala ngati mmene ankayembekezera. A Mboniwo atamuwerengera malemba olimbikitsa, iye anawayamikira kwambiri.
Wapolisi wina amenenso ankapita kumisonkhano yathu ali wachinyamata anabwera pakashelefu. Iye anauza abale kuti wasangalala kwambiri kuwaona chifukwa amukumbutsa nthawi imene ankapita kumisonkhano. Iwo anamuuza kuti akhoza kupita kukasonkhana kudera lomwe amakhala ndiponso anamuuza nthawi imene misonkhano yathu imayamba kumeneko. Anasangalalanso kwambiri atalandira Baibulo ndi kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Kenako wapolisiyo ananena kuti wasangalala kwambiri kukumananso ndi a Mboni za Yehova.
Mtsikana wina wazaka 19 amene anakumana ndi mlongo wina pakashelefu ananena kuti chaposachedwapa anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize kumvetsa bwino Baibulo. Mlongoyu atamupempha kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo, iye anavomera mosangalala. Kenako pa tsiku lomwelo, mlongoyu anayamba kuphunzira naye Baibulo ndipo akupitiriza mpaka pano.
Tikuthokoza kwambiri abale ndi alongo athu ku Chile omwe anagwira nawo ntchito yapadera yolalikira imeneyi. Zotsatira za ntchito imene abale ndi alongowa aigwira mwakhama ndi umboni wakuti Yehova akupitiriza kudalitsa anthu omwe akumufunafuna.—Yesaya 55:6.