Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba yomwe muli Khoti Lalikulu Kwambiri ku Santiago, Chile

DECEMBER 31, 2019
CHILE

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Chile Lapereka Chigamulo Chosaiwalika

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Chile Lapereka Chigamulo Chosaiwalika

Pa 13 December, 2019, khoti lalikulu kwambiri ku Chile linasintha chigamulo chomwe khoti laling’ono linapanga ndipo linanena kuti wa Mboni za Yehova wina ali ndi ufulu wokana kuikidwa magazi chifukwa cha chikhulupiriro chake.

Mlongo Ríos wanyamula chikalata cha chigamulo cha khoti chomwe chinaperekedwa pa 13 December, 2019

Chigamulochi chinali chokhudza mlongo wathu wina dzina lake Polonia Ríos yemwe chipatala china chinakana kumupanga opaleshoni chifukwa choti anakana kuikidwa magazi. Mlongoyu anakadandaula za nkhaniyi ku khoti. Pa 6 August, 2019, Khoti la Apilo ku San Miguel linagamula mokomera chipatalacho.

Zitatero, Mlongo Ríos anakachita apilo ku Khoti Lalikulu Kwambiri m’dzikolo ndipo linagamula momukomera. Aka n’koyamba kuti Khoti Lalikulu Kwambiri m’dzikoli lipereke chigamulo choteteza ufulu wa odwala achikulire omwe akana kuikidwa magazi chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Kwa zaka zoposa 25, Khotili lakhala likunena kuti wodwala sangaloledwe kukana chithandizo chomwe madokotala aona kuti n’choyenera kuti apatsidwe pofuna kupulumutsa moyo wake.

Mbali ina ya chigamulo cha Khotili inati: “A Polonia Ríos omwe akudandaula za nkhaniyi . . . ndi wodwala yemwe akufuna kukhala ndi moyo komanso thanzi labwino ngati atapangidwa opaleshoni imene wakhala akuiyembekezera kwa zaka zitatu . . . [Iwo akukana kuikidwa magazi] chifukwa choti ali ndi zifukwa zabwino zokanira kuikidwa magazi ndipo alibe cholinga chilichonse chofuna kuletsa madokotala kuti asawathandize. M’malomwake, akuchita zimenezi chifukwa cha zimene amakhulupirira zomwe tiyenera kuzilemekeza mogwirizana ndi ufulu wa chikumbumtima komanso wolemekeza maganizo awo. Ndipotu tili ndi zifukwa zomveka zololera zimene wasankha chifukwa pali malipoti abwino osonyeza kuti opaleshoniyi ikhoza kuyenda bwino kwambiri popanda kuika magazi.”

Tikusangalala kwambiri limodzi ndi abale athu ku Chile chifukwa cha chigamulo chosangalatsa kwambiri chimenechi.—1 Akorinto 12:26.