Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 15, 2015
CHILE

A Mboni Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Chile

A Mboni Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Madzi Osefukira ku Chile

Nyumba ya Ufumu ku Copiapó inawonongeka kwambiri ndi madzi osefukira komanso matope.

SANTIAGO, Chile—Pa March 25, 2015, mvula yambiri inagwa m’dera la Atacama kumpoto kwa dziko la Chile ndipo inachititsa kuti madzi asefukire n’kuwononga zinthu zambiri. Anthu oposa 30,000 anakhudzidwa ndi ngoziyi. Anthu pafupifupi 25 anafa ndipo ena pafupifupi 3,000 nyumba zawo zinawonongekeratu moti akukhala m’matenti. Padutsa zaka 80 kuchokera pamene mvula inawononga zinthu kwambiri chonchi m’derali.

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Chile inanena kuti palibe wa Mboni amene anafa kapena kuvulala kwambiri. Komabe nyumba 7 za a Mboni zinagwa ndipo zambiri zinawonongeka. Nyumba ya Ufumu imodzi yomwe ndi malo olambirira a Mboni za Yehova inagwa ndipo ziwiri zinawonongeka ndi madzi osefukirawa.

Zinthu zambiri mumzinda wa Diego de Almagro zinawonongeka kwambiri.

A Mboni za Yehova anakonza komiti yothandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi mumzinda wa Copiapó, womwe ndi umodzi mwa mizinda imene inakhudzidwa kwambiri ndi mvulayi. Komitiyi inkafufuza anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi komanso inakhazikitsa ntchito yochotsa matope ndi zinyalala. Woimira ofesi ya a Mboni m’dzikoli anatumizidwa kuti akathandize ndi kulimbikitsa a Mboni a m’derali. Ngoziyi itangochitika, a Mboni a m’mizinda ya Antofagasta, Arica, Calama, Caldera, Iquique ndi La Serena anatumiza katundu kuti athandize a Mboni anzawo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi.

A Mboni akupakira katundu pa Nyumba ya Ufumu ya mumzinda wa Alto Hospicio woti akathandizire anthu okhudzidwa ndi madzi osefukira.

Bambo Jason Reed, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Chile ananena kuti: “Tikumvera chisoni anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi ndipo komiti imene takhazikitsayi ikuthandiza mwakhama pa ntchito yochotsa zinyalala ndi matope komanso pa ntchito yomanganso nyumba zimene zinagwa. Tikuyesetsanso kulimbikitsa aliyense amene wakhudzidwa ndi madzi osefukirawa.”

Lankhulani Ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Chile: Jason Reed, tel. +56 2 2428 2600