JANUARY 30, 2017
COLOMBIA
A Mboni Anapatsidwa Mphoto ndi Bungwe Loona Ntchito Yomasulira M’chinenero cha Manja ku Colombia
BOGOTA, Colombia—Pa msonkhano womwe unachitika pa October 7 mpaka 9, 2016, ku Colombia, a bungwe loyang’anira ntchito zosiyanasiyana zokhudzana ndi kumasulira zinthu m’chinenero chamanja, (The National Association of Sign-Language Translators/Interpreters and Interpreter Guides of Colombia) ANISCOL, limodzi ndi mabungwe ena awiri, anapereka mphoto kwa a Mboni za Yehova chifukwa chomasulira mabuku ndi zinthu zina m’chinenero chamanja. Aka kanali koyamba kuti bungweli lichititse msonkhano wa anthu omwe amamasulira zinthu m’chinenero chamanja, zomwe zimathandiza kwambiri anthu omwe ali ndi vuto lakumva komanso kuwona.
A Mboni za Yehova anaitanidwa kuti akalandire mphoto chifukwa cha “ntchito yotamandika yomwe amagwira pomasulira zinthu za chipembedzo m’chinenero chamanja zomwe zikuthandiza kwambiri anthu amene ali ndi vuto losamva ku Colombia.” A Ricardo Valencia Lopez amene anakonza nawo msonkhanowu, omwenso ndi a pulezidenti a bungwe linanso loona za ntchito yomasulira m’chinenero chamanja, (Association of Interpreters, Interpreter Guides, and Translators of Colombian Sign Language in the Coffee Axis) ASINTEC, ananenanso kuti a Mboni za Yehova anaitanidwa chifukwa “chothandiza nawo pa ntchito yopititsa patsogolo ntchito yomasulira m’chinenero chamanja. Zinthu zimene amamasulira zimasonyeza kuti ali ndi luso kwambiri pa ntchitoyi ndipo anthu enanso angaphunzireko mmene angagwirire ntchitoyi.”
Pa msonkhanowu, a Mboni anafotokoza momveka bwino zimene zimachitika akamagwira ntchito yawo. Komiti ya msonkhanowu inachita chidwi kwambiri ndi zimene anafotokozazo ndipo inapereka mphoto inanso kwa a Mboniwo pambuyo pomvetsera zinthu zosangalatsa zimene anafotokoza.
A Cristian David Valencia ochokera ku Pereira omwe amapanga mapulogalamu a zinthu zojambulidwa anapezekanso pa msonkhanowu. Iwo ananena kuti “anadabwa kwambiri kuona kuti gulu la chipembedzo lili ndi ndondomeko yabwino kwambiri yophunzitsira anthu omwe ali ndi vuto losamva,” makamaka podziwa kuti a Mboni salipiridwa chifukwa cha ntchito yomwe amagwira.
A Wilson Torres omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Colombia anati: “Tinayamba kupanga zinthu za anthu a vuto losamva kuyambira mu 2000. Panopa pa webusaiti yathu pokha, pali mavidiyo oposa 400 omwe ndi othandiza akuluakulu, achinyamata, komanso ana amene amagwiritsa ntchito zinthu za m’Chinenero Chamanja cha ku Colombia. Tipitirizabe kupanga zinthu za m’chinenero chamanja zofotokoza nkhani za m’Baibulo kwaulere ngati mmene takhala tikuchitira ndi mabuku ena onse.”
Pa dziko lonse, a Mboni za Yehova amene amagwira ntchito yomasulira amapanga mavidiyo a zinthu zosiyanasiyana zomwe timafalitsa m’zinenero zamanja zokwana 88. A Mboni za Yehova anapanganso pulogalamu ya JW Library ya Chinenero Chamanja yomwe imathandiza anthu kupanga dawunilodi mavidiyo a m’chinenero chamanja, kuwaika m’malo omwe akufuna komanso kuonera mavidiyowa kudzera pa webusaiti ya jw.org.
Lankhulani ndi:
International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000
Colombia: Wilson Torres, +57-1-8911530