6 FEBRUARY 2024
CUBA
Mabuku a Mateyu ndi Maliko Anatulutsidwa M’chinenero Chamanja cha ku Cuba
Pa 20 January 2024, mabuku a Mateyu ndi Maliko anatulutsidwa m’Chinenero Chamanja cha ku Cuba pamsonkhano wapadera womwe unachitikira ku Malo a Msonkhano a Guanabacoa ku Havana m’dziko la Cuba. Nthawi yomweyo mabukuwa anayamba kupezeka pa jwo.org kuti anthu achite dawunilodi.
M’dziko la Cuba muli anthu a vuto losamva pafupifupi 53,000. Chakumayambiriro kwa chaka cha 1990, ku Cuba kunachitika ntchito yapadera yolalikira kwa anthu a vuto losamva. Mabuku oyamba a Chinenero Chamanja cha ku Cuba anatulutsidwa mu 2011. Panopa m’dziko la Cuba muli abale ndi alongo 756 omwe akutumikira mumipingo 28 ya ndi magulu 10 a Chinenero Chamanja.
Aka ndi koyamba kuti mabuku a Mateyu ndi Maliko amasuliridwe m’Chinenero Chamanja cha ku Cuba. Mlongo wina ananena kuti: “Nkhani ya pa Maliko 7:32-37 yofotokoza mmene Yesu anachiritsira munthu wa vuto losamva inamasuliridwa bwino kwambiri moti ineyo ndikuchita kumva ngati Yesu ankachiritsa ineyo. Inandifika pamtima n’saname. Panopa sindingavutike kuganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Zikomo kwambiri!”
Tikusangalala limodzi ndi onse omwe analandira mphatso yapaderayi kuchokera kwa Yehova. Ndipo tikukhulupirira kuti anthu ambiri amene amagwiritsa ntchito Chinenero Chamanja cha ku Cuba apitiriza kukonda kwambiri Yehova ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse, komanso maganizo awo onse.—Maliko 12:30.