Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 11, 2019
CZECH REPUBLIC

A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso la Chitcheki ndi la Chisilovaki

A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso la Chitcheki ndi la Chisilovaki

Pa 7 September, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso linatulutsidwa m’zinenero za Chitcheki ndi Chisilovaki. M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira ndi yemwe anatulutsa Mabaibulowa pamsonkhano wapadera womwe unachitikira mumzinda wa Ostrava ku Czech Republic. Anthu ena anamvetsera msonkhanowu kuchokera m’malo oposa 200 a ku Czech Republic ndi ku Slovakia, ndipo chiwerengero cha onse omwe anapezeka pamsonkhanowu chinali 25,284.

Ntchito yomasulira Mabaibulowa inagwiridwa ndi magulu awiri a omasulira ndipo gulu lililonse linagwira ntchitoyi kwa zaka zoposa 4. Ubwino waukulu wa Mabaibulo okonzedwansowa ndi woti ndi osavuta kuwerenga. Mmodzi mwa anthu omwe anamasulira nawo Baibulo la Chisilovaki anati: “Anthu ambiri azisangalala kwambiri akamawerenga Baibuloli. Mawu omwe agwiritsidwa ntchito ndi osavuta kuwerenga komanso kumvetsa zomwe akutanthauza. Zimenezi zizichititsa owerenga kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa mmene nkhani yomwe akuwerenga inathera, ndipo kuzikhala kovuta kuti asiye kuwerenga nkhaniyo.”

A Mboni za Yehova omwe apindule ndi Mabaibulowa ndi oposa 15,000 a ku Czech Republic komanso oposa 11,000 a ku Slovakia. Mmodzi mwa anthu omwe anamasulira nawo Baibulo la Chitcheki anafotokoza kuti: “Cholinga chachikulu cha Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso ndi kumasulira mfundo za m’chiyankhulo choyambirira chomwe Baibulo linalembedwamo pogwiritsa ntchito ziganizo zazifupi komanso chinenero chamakono. Achinyamata komanso anthu omwe angoyamba kumene choonadi azilimvetsa bwino Baibulo, osati anthu okhawo omwe akhala m’choonadi kwa nthawi yayitali.”

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’zinenero 184, kuphatikizapo Mabaibulo a zinenero 29 omwe akonzedwanso mogwirizana ndi la Chingelezi lomwe linatulutsidwa mu 2013. Ndi pemphero lathu kuti anthu omwe aziwerenga Mabaibulowa awathandize kukonda kwambiri choonadi cha m’Baibulo.—Luka 24:32.