Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 24, 2020
DEMOCRATIC REPUBLIC OF THE CONGO

A Mboni za Yehova M’gawo la Nthambi ya ku Congo (Kinshasa) Akuvutika Ndi Mliri, Madzi Osefukira Ndiponso Nkhondo

A Mboni za Yehova M’gawo la Nthambi ya ku Congo (Kinshasa) Akuvutika Ndi Mliri, Madzi Osefukira Ndiponso Nkhondo

Abale ndi alongo m’madera ena a m’dziko la Democratic Republic of the Congo komanso Republic of the Congo akuvutika ndi mliri wa koronavairasi, madzi osefukira komanso nkhondo. Ofesi ya nthambi ya ku Congo (Kinshasa), yomwe imayang’anira ntchito yolalikira m’mayiko awiriwa, yakonza zoti abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi mavutowa apatsidwe zinthu zina zofunikira komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo. Ofesi ya nthambiyi yapanga makomiti othandiza pakagwa mavuto amwadzidzidzi (omwe mwachidule amatchedwa DRC) m’madera omwe akhudzidwa ndi mavutowa kuti azipereka thandizo kwa abale. Pofika pano, abale ndi alongo okwana 90,000 alandira kale chakudya.

Pa 16 ndi pa 17 April, 2020, mvula yamphamvu inagwa n’kuchititsa kuti m’madera akum’mawa kwa dziko la Democratic Republic of the Congo kusefukire madzi. Zimenezi zinachititsa kuti abale ndi alongo okwana 139 achoke kumene ankakhala. Panopa anthuwa akusungidwa m’makomo mwa abale ndi alongo awo. Makomiti a DRC amene ali m’derali akugwira ntchito mwakhama kuti apezere anthuwa malo okhala ndipo ena akuwamangira nyumba.

Abale ndi alongo akumapereka zinthu zawo mowolowa manja pothandiza makomiti amenewa. Mwachitsanzo m’dera lina, abale ndi alongo anapereka 700kg ya nthochi, 400kg ya chimanga, ndi 220kg ya chinangwa komanso chigwada.

Kuwonjezera pamenepo, ofalitsa 60 a mpingo wa Some 26 Km analandira m’nyumba zawo abale ndi alongo 50 omwe anathawa nkhondo. Ofalitsawa ankagawira anzawowo chakudya kufikira pamene abale a DRC anapereka thandizo la chakudya.

M’bale wina ku Brazzaville, lomwe ndi likulu la dziko la Republic of the Congo, anafotokoza zotsatirazi atalandira thandizoli: “Zinthu zimasintha pa moyo wa munthu nthawi iliyonse. Poyamba ndinkagwira ntchito ndipo ndinkalandira malipiro abwino ndithu. Mkazi wanganso ankagwira timaganyu moti sitinkavutika kupeza zofunikira pamoyo. Ndiyeno matenda a COVID-19 atayamba, makomo onse a ndalama anatsekeka. Koma zimenezi sizinachititse kuti tisiye kudalira Yehova. Zinangochitika kuti pamene tinkakambirana kuti tipanga bwanji chakudya chikatithera, Yehova analowererapo.”

Mlongo wina wamasiye yemwe amakhala ku Kinshasa, dzina lake Mbuyi Ester, anafotokozanso zofanana ndi zimenezi. Iye anati: Mwamuna wanga anamwalira mwezi wapitawo ndipo ndinalibiretu pogwira. Sindinkagwira ntchito komanso ndinali ndi ana atatu ofunika kuwadyetsa. Achibale anga sakanakwanitsa kutipatsa chakudya chochuluka chonchi, chokwanira kudya masiku ambirimbiri. Zikomo kwambiri Yehova!”

Ndi pemphero lathu kuti Yehova apitirize kusamalira abale ndi alongo amenewa komanso kudalitsa ntchito yopereka chithandizoyi. Tikuyembekezeranso mwachidwi pa nthawi imene aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira.—Salimo 72:16.