31 MAY 31, 2021
DEMOCRATIC REPUBLIC OF THE CONGO
Anthu Masauzande Asamuka Chifukwa cha Kuphulika kwa Phiri ku Goma
Malo
Goma, ku Democratic Republic of the Congo
Ngozi yake
Loweruka pa 22 May 2021, Phiri la Nyiragongo linaphulika ku chigawo cha North Kivu pafupi ndi mzinda wa Goma ndipo izi zinachititsa kuti anthu masauzande ambiri asamuke kwawo
Mmene zakhudzira abale ndi alongo athu
Ofalitsa 2,000 anasamukira m’mizinda yapafupi
Abale ndi alongo okwana 35 amene ali mu utumiki wapadera anasamukanso kwa kanthawi
Katundu amene wawonongeka
Nyumba pafupifupi 29 za abale ndi alongo zinawonongeka
Ntchito yothandiza anthu
Komiti yothandiza anthu (DRC) inakhazikitsidwa kuti iziyang’anira ntchito yopereka chithandizo. Komitiyi ikugwira ntchito limodzi ndi oyang’anira madera komanso akulu kuti ione zinthu zimene zawonongeka komanso kuthandiza abale ndi alongo amene akhudzidwa.
Aliyense akuyesetsa kutsatira njira zopewera matenda a COVID-19 pothandiza anthu
N’zoona kuti nyumba za abale ndi alongo ena zinawonongeka koma tikusangalala kuti palibe ngakhale mmodzi amene wavulala chifukwa cha ngoziyi. Tikupitiriza kuwapempherera pamene akudalira Yehova pa nthawi yovutayi.—Nahumu 1:7.