Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mapu osonyeza madera a North Kivu ndi Ituri komwe matenda a Ebola afalikira kwambiri. Mtsikana wamng’ono akusamba m’manja pamalo osambira m’manja omwe anaikidwa pamsonkhano wadera ku Beni.

MAY 2, 2019
DEMOCRATIC REPUBLIC OF THE CONGO

Matenda a Ebola Akupitiriza Kupha Anthu Ambiri ku Democratic Republic of the Congo

Matenda a Ebola Akupitiriza Kupha Anthu Ambiri ku Democratic Republic of the Congo

Kuyambira mu August 2018, pamene anthu ku Democratic Republic of the Congo akhala akumenyana komanso kuchita zionetsero, anthu ambiri akhala akugwidwa ndi matenda a Ebola. M’madera a North Kivu komanso Ituri, anthu oposa 1,088 agwidwa ndi Ebola ndipo anthu 665 afa ndi matendawa. N’zomvetsa chisoni kuti abale athunso akhudzidwa ndi matendawa. Ofesi ya nthambi ya Congo (Kinshasa) yanena kuti pa a Mboni za Yehova omwe akhudzidwa, ana awiri ndiponso akuluakulu 10 afa ndi matendawa. M’bale wina anagwidwa ndi matendawa koma anachira.

Pofuna kuphunzitsa abale mmene angapewere matendawa, ofesi ya nthambi ya Congo (Kinshasa) inalandira chilolezo kuchokera ku Komiti ya Ogwirizanitsa kuti akonze vidiyo komanso nkhani yapadera. Vidiyoyi inali ndi malangizo othandiza. Mwachitsanzo, inanena kuti zingakhale bwino ngati mipingo yonse itakhala ndi malo oti anthu azisamba m’manja akafika kumisonkhano, ndipo tsopano mipingo yonse ikutsatira malangizowa. Zimenezi zathandiza kuchepetsa kufalikira kwa matendawa. Chifukwa cha zimenezi, akuluakulu a zaumoyo anatumiza makalata ku ofesi ya nthambi oyamikira chitsanzo chabwino komanso mgwirizano umene a Mboni za Yehova asonyeza pa nthawi yomwe m’dzikolo mwabuka matenda a Ebola.—Mateyu 5:16.

M’mizinda yambiri, abale athu akhala asakuchoka m’nyumba zawo kwa milungu ingapo poopa kupatsirana matendawa. Pofuna kuchepetsa kufalikira kwa matendawa pa nthawi yoopsayi, ofesi ya nthambi yapempha madera 12 kuti asachite kaye misonkhano yawo yachigawo. Pofuna kuonetsetsa kuti abalewa akulandirabe chakudya chauzimu, ofesi ya nthambi yakonza zoti mipingo yokhudzidwa ionere vidiyo yochita kujambulidwa ya pulogalamu ya msonkhanowu m’Nyumba za Ufumu zawo.

Tikupempherera abale ndi alongo athu ku Democratic Republic of the Congo. Timalimbikitsidwa ndi chiyembekezo chopezeka m’Baibulo choti m’tsogolomu matenda adzathetsedwa.—Yesaya 33:24.