Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mmene maofesi atsopano a ku Lubumbashi, Democratic Republic of the Congo azidzaonekera

21 JANUARY, 2022
DEMOCRATIC REPUBLIC OF THE CONGO

Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Democratic Republic of the Congo Ili Mkati

Ntchito Yomanga Ofesi ya Nthambi Yatsopano ku Democratic Republic of the Congo Ili Mkati

Ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ili mkati ku Lubumbashi m’dziko la Republic of the Congo. Imeneyi ndi imene idzakhale ofesi yaikulu m’dzikolo. Atumiki a Pabeteli okwana 260, akuyembekezeka kudzasamukira ku ofesi yatsopanoyi cha mu May 2022. Atumiki ena okwana 131 adzapitirizabe kukhala ku ofesi yakale yomwe ili ku Kinshasa. a Ntchito yomanga nyumba zogonamo komanso maofesi owonjezera pa nthambi yakale ya ku Kinshasa, inayambika. Atumiki a pabeteli okwana 48 adzayamba kukhala m’nyumba zatsopanozi cha kumapeto kwa January 2024. Maofesi awiri onsewa adzathandiza kupititsa patsogolo ntchito za Ufumu zomwe zikuwonjezereka m’dziko la Congo.

Ntchito yomanga ofesi imodzi pa maofesi atatu omwe adzakhale pamalowa, ili mkati

M’chaka chautumiki cha 2021, abale a ku Democratic Republic of the Congo anachititsa maphunziro a Baibulo opitirira 250,000. Anthu oposa 1 miliyoni anapezeka pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu. Panopo, abale ndi alongo okwana 394, ndi omwe akutumikira pabeteli ya ku Kinshasa.

Popeza sizikanatheka kuwonjezera ofesi ya nthambi ya ku Kinshasa, abale anayamba kufufuza malo m’mizinda ina kuti amangepo. Pamapeto pake anapeza malo aakulu bwino ku Lubumbashi okwanira kumangapo ofesi ya nthambi yatsopano komanso maofesi ena owonjezera ngati angadzafunike m’tsogolo.

Kumanzere: Posachedwapa Atumiki a Pabeteli pafupifupi 300, asamukira ku ofesi yatsopano ya ku Lubumbashi. Kumanja: Mmene malowa adzaonekere ntchitoyi ikadzatha

Malo a ku Lubumbashi ali pamtunda wa makilomita 2,300 kuchokera ku Kinshasa. Malowa ndi okwana mahekitala 12 ndipo padzakhala nyumba zogonamo, maofesi, nyumba yosungiramo katundu, chipinda chokhala ndi malo odyera chomwe chizidzagwiritsidwanso ntchito kuchitiramo zinthu zosiyanasiyana komanso malo osewerera.

Ntchito yomanga pamalowa inayamba mu November 2020, komabe yakhala ikukumana ndi mavuto ena chifukwa cha mliri wa COVID-19.

M’bale Robert Elongo amene akutumikira mu Komiti ya Nthambi ya Congo (Kinshasa), anafotokoza kuti: “Maboda anali otseka ndipo zimenezi zinakhudza kwambiri ntchito yoitanitsa zipangizo zomangira. Chifukwa cha vutoli, chigawo choyamba cha ntchitoyi chitenga nthawi yaitali kuti chithe.”

Ngakhale zinali choncho, M’bale Elongo ananena kuti: “M’chaka chimodzi choka pafupifupi hafu ya chigawo choyamba cha ntchitoyi chinamalizidwa.”

N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchitoyi. Ndi pemphero lathu kuti Ofesi yatsopanoyi ithandiza poperekera umboni kwa anthu a m’dzikoli komanso kuthandiza kuti dzina la Yehova lilemekezedwe.—Mateyu 24:47.

a Ofesi ya nthambi ya Democratic Republic of the Congo (Kinshasa), imayang’anira ntchito za Ufumu m’gawo la Democratic Republic of the Congo ndi Republic of the Congo.