Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

25 JULY, 2017
DEMOCRATIC REPUBLIC OF THE CONGO

A Mboni za Yehova Anapereka Chithandizo kwa Anthu Othawa Nkhondo ku Congo

A Mboni za Yehova Anapereka Chithandizo kwa Anthu Othawa Nkhondo ku Congo

A Belinda (sititchula dzina la bambo awo pofuna kuwateteza) ali ndi ana awo atatu m’chipatala ku Dundo m’dziko la Angola. Mwamuna wawo anaphedwa ku Congo, ndipo mwana wawo wina wamkazi akusowa. A Belinda limodzi ndi mwana wawo wamng’ono wamkazi anavulala atawomberedwa. Mwanayo dzina lake ndi Ritinha ndipo ali ndi zaka ziwiri. Panopo madokotala akufunika kudula miyendo yonse ya Ritinha. Mwana wina wa a Belinda anavulala koopsa anthu ena atamutema ndi zikwanje.

KINSHASA, Congo—A Mboni za Yehova anapereka zinthu zosiyanasiyana zothandizira abale awo amene akuvutika chifukwa cha nkhondo imene ikuchitika m’chigawo cha Kasai m’dziko la Democratic Republic of Congo. Iwo anawalimbikitsanso ndi uthenga wa m’Baibulo. Anthu m’dzikolo akhala akuvutika ndi nkhondo yapachiweniweni, zipolowe komanso magulu a zigawenga. Anthu oposa 1.3 miliyoni anathawa m’dzikolo kuphatikizapo anthu 30,000 a m’chigawo cha Kasai omwe anathawira m’dziko la Angola. Ambiri mwa anthuwa anachitiridwa nkhanza zoopsa ndipo atafika ku Angola anafunika chithandizo cha mankhwala. Ena anawotchedwa kwambiri komanso anali ndi mabala oopsa a zikwanje komanso zipolopolo. Malipoti akusonyeza kuti a Mboni za Yehova oposa 870 anathawira ku Angola limodzi ndi ana awo ang’onoang’ono ndipo a Mboni pafupifupi 10 anavulazidwa. N’zomvetsa chisoni kuti a Mboni za Yehova okwana 22 anaphedwa pa nkhondoyo.

M’modzi mwa anthu amene anatumizidwa ndi ofesi ya Mboni za Yehova ku Angola akucheza ndi akulu ena a ku Angola ndi ku Congo, ndipo ena mwa akuluwo ndi othawa kwawo.

A Robert Elongo, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku ofesi yawo ku Kinshasa ananena kuti: “N’zomvetsa chisoni kwambiri kuti anthu ambiri aphedwa pankhondoyi ndipo ambiri mwa anthuwa ndi ana aang’ono. Ena anaphedwa chifukwa chokhala kufupi ndi madera omwe kunayambika nkhondo mwadzidzidzi. Tikudera nkhawa kwambiri abale anthu ndipo tawalangiza kuti azichita zinthu mosamala. Ifeyo limodzi ndi abale athu ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Angola tikuyesetsa zimene tingathe kuthandiza abale anthu ndi zinthu zofunika komanso kuwalimbikitsa mwauzimu.”

Anthu omwe anathawa nkhondo ku Congo akufolela kanyumba.

A Mboni za Yehova ku Angola ndi ku Congo akhazikitsa makomiti othandiza anthu pa ngozi zadzidzidzi kuti athandize anthu amene akuvutika ndi nkhondoyo. Mwachitsanzo anatumiza katundu wolemera matani 34 amene abale anapereka kuti akathandize abale awo. Wina mwa katunduyo ndi mabulangete, zovala, zakudya, maneti, nsapato komanso mankhwala olemera makilogalamu 525. Dokotala wina yemwenso ndi wa Mboni za Yehova anapita kumalo a anthu othawa kwawowo kuti akathandize anthu 135 omwe akufunika chithandizo mwansanga.

Komanso anthu ochokera ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Angola ndi ku Congo anapita kumalowa kuti akalimbikitse abalewo. Atafika anachititsa misonkhano yapadera pomwe anakamba nkhani zochokera m’Baibulo zokhala ndi mfundo zolimbikitsa mogwirizana ndi mavuto amene akukumana nawo. Ngakhale kuti anthu ambiri ku Angola amalankhula Chipwitikizi, misonkhano yophunzira Baibulo imachitika m’Chiluba chomwe ndi chimodzi mwa zilankhulo 4 zikuluzikulu kwambiri ku Congo. Anachita zimenezi kuti anthu othawa kwawowo apindule ndi misonkhanoyo monga mmene chithunzi chili pamwambachi chikusonyezera.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lomwe lili ku likulu lawo lapadziko lonse ndi limene limayang’anira ntchito yopereka chithandizo. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka pothandizira ntchito yophunzitsa anthu Baibulo padziko lonse.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Angola: Todd Peckham, +244-923-166-760

Democratic Republic of the Congo: Robert Elongo, +243-81-555-1000