Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya 2018 Iyamba mu May

Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya 2018 Iyamba mu May

NEW YORK—Lachisanu pa 18 May, 2018, a Mboni za Yehova adzayamba kuchita misonkhano yawo yachigawo yomwe imachitika chaka chilichonse. Msonkhano wa chaka chino uli ndi mutu wakuti: “Limbani Mtima.” Misonkhanoyi isanayambe, a Mboni padziko lonse azigwira ntchito yoitanira anthu kuti adzapezeke nawo pa misonkhanoyi yomwe ndi yaulere. Misonkhanoyi idzachitika m’malo osiyanasiyana m’mayiko okwana 180.

Msonkhanowu ndi wa masiku atatu ndipo padzakhala nkhani, masewero omvetsera, kucheza ndi anthu ena komanso timavidiyo. Komanso pa tsiku lomaliza la msonkhanowu padzaonetsedwa vidiyo ya mutu wakuti: Nkhani ya Yona—Yophunzitsa Kulimba Mtima Komanso Chifundo. Tsiku lililonse chigawo cham’mawa ndi chamasana chizidzayamba ndi mavidiyo a nyimbo zomwe zakonzedwa mwapadera kuti ndi za msonkhano wachigawo.

A David A. Semonian omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova anati: “Masiku ano ukamaonera kapena kuwerenga nkhani, umaoneratu kuti anthu amisinkhu yonse akulimbana ndi mavuto osiyanasiyana komanso zinthu zoopsa kusiyana ndi kale lonse. Kuti munthu athe kupirira mavutowa amafunika kukhala wolimba mtima. Choncho tikuitana aliyense kuti adzakhale nawo pamsonkhano wachigawo wa chaka chino n’cholinga choti adzapindule ndi malangizo othandiza amene amapezeka m’Baibulo.”

Kuti mudziwe malo ndi masiku a msonkhano uliwonse, onani pa webusaiti yovomerezeka ya Mboni za Yehova ya jw.org.

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000