Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuyambira kumanzere kupita kumanja: Ofalitsa a ku Germany, Mexico ndi South Africa

14 SEPTEMBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Ayambiranso Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba

A Mboni za Yehova Ayambiranso Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba

Atayembekezera kwa nthawi yaitali kuti ayambirenso kulalikira kunyumba ndi nyumba, pa 1 September 2022, a Mboni za Yehova padziko lonse anayambiranso kugwira ntchitoyi yomwe amadziwika nayo kwambiri. Ntchito yapadera yoyambitsa maphunziro a Baibulo yomwe ikuchitika m’mweziwu, yathandiziranso kuti utumikiwu ukhale wosangalatsa kwambiri. Kwa abale ndi alongo ena, kumeneku kunali kuyambiranso kuchita utumiki womwe anauzolowera komanso kuukonda kwambiri. Ndipo kwa ena, imeneyi inali nthawi yoyamba kukumana pamasom’pamaso ndi maneba awo kuti awauze uthenga wa m’Baibulo. Zotsatirazi ndi zina mwa zinthu zosangalatsa zomwe abale athu akumana nazo padziko lonse pomwe chaka chautumiki cha 2023 chinkayamba.

Germany

Pa 2 September 2022, Nicole ndi Tina, alongo a ku Petershagen ku North Rhine-Westphalia ankalalikira kunyumba ndi nyumba koma sanapeze aliyense pakhomo. Akubwerera, anamva mayi wina wachitsikana akuwaitana. Mayiyo anauza alongowo kuti anawamva akugogoda koma sakanakwanitsa kuti awatsegulire ndipo anawapempha kuti alowe kuti akambirane nkhani ya m’Baibulo. Alongowo atalowa, anapeza kuti mayiyo anali ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika patebulo lake. Mayiyo anafotokoza kuti anapatsidwa Baibulolo pomwe ankakhala ku Italy zaka zitatu zapitazo. Koma atasamukira ku Germany pa nthawi ya mliri, sanakhalenso ndi mwayi wokumana ndi a Mboni za Yehova. Alongowa anapatsana manambala a foni ndi mayiyu komanso anamuitanira kumisonkhano yathu. Patatha masiku awiri, mayiyo limodzi ndi ana ake awiri anabweradi kumsonkhano wampingo. Alongowa anakambirana naye zoyamba kuphunzira Baibulo.

Guatemala

Manuel ndi Karol Gastelum omwe akutumikira ngati apainiya apadera m’gawo lolankhula Chimamu, anakumana ndi mayi wina wokoma mtima yemwe anawaitanira m’nyumba mwake. Mayiyo sankadziwa kuti Mulungu ali ndi dzina choncho anayamba kukambirana naye phunziro 04 lakuti “Kodi Mulungu Ndi Ndani?” m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Atawerenga naye lemba la Yesaya 42:8, mayiyo anadabwa kuona kuti m’Baibulo lake munali dzina la Mulungu lakuti Yehova.

Mayi uja anayamba kulira n’kunena kuti wazindikira kuti kungokhala ndi Baibulo sikokwanira ndipo anati akufuna kuliphunzira kuti azichita zinthu zogwirizana ndi zomwe limaphunzitsa. Pamapeto pake mayiyo anathokoza kwambiri banjali chifukwa cha zomwe anaphunzira. Mayiyo anati akauzanso mwamuna wake zomwe waphunzirazo. Banja la a Gastelum linapangana ndi mayiyu kuti apitirize kuphunzira naye Baibulo.

Japan

Pomwe M’bale ndi Mlongo Nukamori anali mu utumiki, anafika pa nyumba ina pomwe pali intakomu. Kenako anamva mawu a munthu wamkazi akuwapatsa moni. Iwo anauza munthuyo kuti ndi a Mboni za Yehova. Mayiyo anauza banjali kuti liwadikire pakhomo pomwepo. Patapita kanthawi, mayi uja anatsegula chitseko n’kuwauza kuti, “Ndakhala ndikuyembekezera kuti a Mboni za Yehova abwere.”

Mayiyo anafotokoza kuti anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova pomwe ankakhala ku Nagasaki. Atasamukira ku Yokohama pa nthawi ya mliri anapitiriza kuphunzira kudzera pa Zoom. Kumayambiriro kwa wiki imeneyo, mlongo yemwe ankaphunzira naye anamuuza kuti: “Tidzakhala ndi ntchito yapadera mu September. Sindikukayikira kuti a Mboni za Yehova adzafika pa nyumba panu. Akadzabwera, mudzawapemphe kuti aziphunzira nanu Baibulo pamasom’pamaso.” Mayiyo anasangalala kwambiri kuti sipanapite nthawi yaitali ndipo Amboniwo anafikadi. Ananenanso kuti akufuna kukapezeka nawo pamisonkhano yathu ndiponso anagwirizana zoyamba kuphunzira Baibulo.

Ofalitsa a ku Japan akulalikira khomo ndi khomo

Mexico

Banja lina litapempha mayi wina kuti aziphunzira naye Baibulo, mayiyo ananena kuti anaphunzirapo ndi a Mboni za Yehova komanso ankapezeka pamisonkhano zaka zambiri zapitazo. Nthawi yonseyi sanakumanenso ndi a Mboni za Yehova komanso ankachita manyazi kuti awafufuze chifukwa sankachita zinthu zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Atafotokoza zimenezi, anayamba kulira. Banjali linamuwerengera lemba la Salimo 10:17 n’kumutsimikizira kuti Yehova sanamuiwale. Anamuyamikiranso chifukwa chokhala ndi mtima wofunitsitsa kutsatira mfundo za Yehova. Anavomera zoyambiranso kuphunzira Baibulo ndipo ananenanso kuti mwana wake wamwamuna wazaka 16 nayenso akufuna kudziwa zambiri zokhudza Baibulo.

Mawa lake banja lija litabweranso, linapeza mayi uja ndi mwana wake akuwayembekezera. Atamaliza kuphunzira phunziro 01 m’kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, banjali linawaitanira kumisonkhano yakumapeto kwa mlungu ndipo anabweradi. Mayi uja ndi mwana wake akufuna kupitiriza kuphunzira komanso kupezeka pamisonkhano.

Puerto Rico

Banja la ku Puerto Rico likugawira mayi wina kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale

Ramon anapemphera kuti apeze munthu amene angamuuze uthenga wabwino pa tsiku loyambiranso kulalikira khomo ndi khomo. Atafika panyumba yoyamba, mayi wina anangotsegula chitseko pang’ono n’kusuzumira. Mwachidule, Ramon anapereka moni n’kufotokoza chomwe anabwerera. Koma asanayambe kumulalikira, mayiyo anamuuza kuti: “Ndakhala ndikuyembekezera nthawi imeneyi. Ndakhala ndikupemphera kuti anthu inu mubwere kunyumba kwanga.”

Mayiyo anafotokoza kuti anakumanapo ndi Amboni zaka zochepa zapitazo ndiponso kuti anapezekapo pamsonkhano wathu wina. Koma atasamuka, sanakumanenso ndi Wamboni aliyense. Ramon anauza mayiyo kuti pa nthawi ya mliri, tinaimitsa kaye ntchito yolalikira kunyumba za anthu. Kenako Ramon anamuwerengera mayiyo lemba la Salimo 37:29 n’kumupempha kuti aziphunzira naye Baibulo ndipo anavomera. Ramon anakonza zoti mlongo wina aziphunzira ndi mayiyu.

Zimenezi zitachitika, Ramon anafotokoza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova ndi angelo ndi omwe akutitsogolera kwa anthu omwe akufuna kumva uthenga.”

United States

Katelyn Thompson atafika pa nyumba ina ku Kentucky, anaona bokosi lolandirira makalata litalembedwa mavesi a m’Baibulo. Komanso pakhomopo panali kachikwangwani kolembedwa kuti, “Yesu amakukondani.” Katelyn atagogoda panyumbapo, mayi wina anayankha. Zitatero, Katelyn analankhula ndi mayiyo n’kumuuza kuti, chifukwa cha mliri wa COVID-19, a Mboni za Yehova sankakumana ndi maneba awo pamasom’pamaso. Anamuuzanso kuti panthawiyi Amboni ankalemba makalata komanso kuimbira anthu mafoni ndi cholinga chofuna kuwalimbikitsa ndi kuwatonthoza. Katelyn anafunsa za moyo wa mayiyo limodzi ndi banja lake. Mayiyo anafotokoza kuti bambo ake anamwalira pa nthawi ya mliri. Ananenanso kuti: “Ndinkalandira makalata anu. Ndipo ndikalandira makalatawo, ndinkaona kuti Mulungu ankandipatsa thandizo lomwe ndinkafunikira panthawiyo.” Katelyn anapepesa mayiyo chifukwa cha zomwe zinamuchitikira ndipo anakambirana naye phunziro 02 m’kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Anawerenganso malemba omwe ali m’phunzirolo ndiponso kukambirana kwambiri za chiyembekezo choti akufa adzauka. Kenako mayiyo anayamba kulira. Mayiyo anafotokoza kuti pofika tsikulo, panali patatha chaka kuchokera pomwe bambo ake anamwalira. Mayiyo anapatsa Katelyn nambala yake yafoni ndipo anagwirizana zoti adzabwerenso. Nthawi ina tsiku lomwelo, Katelyn analandira meseji yochokera kwa mayi uja yakuti: “Ndathokoza kwambiri. Lero ndimafunikiradi munthu woti andilimbikitse.”

N’zoonekeratu kuti Yehova wadalitsadi kuyambiranso kwa ntchito yathu yolalikira khomo ndi khomo komanso ntchito yapadera yoyambitsa maphunziro a Baibulo. Tikuyembekezera kuona kuti ntchitoyi iyenda bwanji.—Yohane 4:35.

 

Bahamas

Cameroon

Panama

Philippines

South Korea

United States