4 APRIL, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
A Mboni za Yehova Ayambiranso Kusonkhana Pamasom’pamaso
Kuyambira pa 1 April 2022, a Mboni za Yehova anayambiranso kuchita misonkhano ya pamasom’pamaso. Nkhawa yonse yomwe abale ndi alongo anali nayo inatha ndipo aliyense anali wosangalala ndipo ena anagwetsa misozi yachisangalalo komanso anaimba nyimbo za Ufumu mosangalala kwambiri.
Kwa ena, inali nthawi yawo yoyamba kupezeka pa Nyumba ya Ufumu.
M’bale wina wa ku Poland, dzina lake Krzysztof Hoszowski ananena kuti: “Inali nthawi yanga yoyamba kupezeka pamsonkhano wa pa Nyumba ya Ufumu. Ndinaphunzira Baibulo kudzera pa vidiyokomfelensi komanso pomwe ndinkabatizidwa, nkhani ya ubatizo inakambidwa pa Zoom. Ndinkadziwa mmene misonkhano yapamasom’pamaso imayendera chifukwa ndinali nditaonerapo mavidiyo ambiri osonyeza mmene misonkhanoyi imakhalira. Koma nditapezeka pamsonkhano wapamasom’pamaso, ndinachita chidwi ndi chikondi komanso kukoma mtima komwe abale ndi alongo ankasonyezana.”
Mu March 2020 kutangogwa mliri wa COVID-19, a Mboni za Yehova anayamba kuchita misonkhano yawo kudzera pazipangizo zamakono. Panopo, amene sangakwanitse kupezeka pamisonkhano pamasom’pamaso, angathe kuchitabe misonkhanoyi kudzera pazipangizo zamakono.
M’bale Neil Campbell wa ku Edinburgh m’dziko la Scotland ananena kuti: “Titangoyamba kuimba nyimbo yoyamba, mumtima mwanga munadzaza ndi chisangalalo chifukwa chomva kuti kwa nthawi yoyamba pambuyo pa zaka ziwiri, ndilinso limodzi ndi abale anga.”
Tikuthokoza kwambiri chifukwa cha mmene Yehova watidalitsira kuti tiyambirenso kuchita misonkhano ya pamasom’pamaso.—Salimo 84:10.
Angola
Armenia
Australia
Czech Republic
Ecuador
Germany
Greece
Guinea
Japan
Kazakhstan
Malawi
Netherlands
Philippines
Romania
Scotland
South Korea
South Sudan
Spain
Thailand