MARCH 26, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
A Mboni za Yehova Padziko Lonse Akugwiritsa Ntchito Njira Zatsopano Polalikira pa Nthawi ya Mliri
Mliri watsopano wa kolonavairasi (COVID-19) wakhudza a Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri. Iwo amayesetsa kumvera malangizo omwe olamulira akupereka uku akupitirizabe kulambira Yehova. M’madera omwe akhudzidwa kwambiri ndi mliriwu, abale ndi alongo athu akupitirizabe kulalikira pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana.
M’bale wina yemwe amakhala mumzinda wa Pisa ku Italy anati: “Zinthu zikutiyendera bwino kwambiri mu utumiki! Poganizira zoti panopa anthu ambiri sakuchoka m’nyumba zawo, ine ndi mkazi wanga tinaonanso manambala a foni a anthu omwe tili nawo m’mafoni mwathu n’kukonza zocheza nawo kudzera pa vidiyokomfelensi. Tili ndi maphunziro a Baibulo ambiri ndiponso maulendo obwereza ndipo tapezanso ena atsopano. Tikumachita utumikiwu kwa maola ambiri ndipo zinthu zikuyenda bwino kwambiri.”
Ku South Korea, mliriwu wachititsa kuti ofalitsa azigwiritsa ntchito pafupipafupi mbali zina zapawebusaiti yathu ya jw.org komanso papulogalamu ya JW Library. Mwachitsanzo, m’bale wina analandira meseji kuchokera kwa munthu wina yemwe poyamba ankaphunzira naye Baibulo koma anasiya kuphunzira naye zaka zitatu m’mbuyomu. Munthuyo ananena kuti mliri woopsawu wamuchititsa kuganizira mozama za chizindikiro cha masiku otsiriza. M’baleyu anagwiritsa ntchito mbali yakuti, “Share Link” yomwe ikupezeka pa JW Library pomutumizira mfundo zokhudza masiku otsiriza kudzera pa meseji. M’baleyu anafotokoza kuti ndi “zolimbikitsa kuona kuti chizindikiro cha masiku otsiriza chimenechi chachititsa kuti anthu ambiri ayambe kufuna kudziwa zambiri zokhudza Mulungu komanso Baibulo.”
Malipoti ambiri ochokera ku nthambi zosiyanasiyana padziko lonse akupereka umboni woti abale ndi alongo athu amaona kuti utumiki ndi wofunika kwambiri. N’zosangalatsa kuona kuti akugwiritsa ntchito “nzeru zopindulitsa” popitiriza kuuza ena uthenga wabwino.—Mika 6:9.
Woyang’anira dera akuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki ku Puerto Rico
Alongo omwe ndi apainiya ku Germany akulembera limodzi makalata atalumikizana pa vidiyokomfelensi
Phunziro la Baibulo lili mkati ku South Korea
Mwamuna ndi mkazi wake ku France akulalikira limodzi kudzera pa telefoni
Mlongo ndi mwana wake akulemba kalata ku Hawaii