APRIL 20, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Abale ndi Alongo Akupereka Zopereka Zawo Kudzera pa Intaneti Chifukwa cha Mliri wa COVID-19
M’mayiko ambiri, abale ndi alongo anasintha zinthu pa nkhani yolalikira komanso kusonkhana chifukwa cha mliri woopsa wa kolonavairasi womwe wakhudza dziko lonse lapansi. M’malo mokumana m’Nyumba za Ufumu, abale ndi alongo akumasonkhana kudzera pa intaneti pogwiritsa ntchito vidiyokomfelensi. Chifukwa cha zimenezi, abale ndi alongo ambiri asinthanso njira zoperekera ndalama zothandizira pa ntchito yolalikira ndipo akumapereka kudzera pa intaneti.
M’mayiko oposa 112, a Mboni za Yehova akhoza kulowa pa webusaiti ya donate.pr418.com n’kupereka ndalama zawo pogwiritsa ntchito makadi awo a kubanki.
Panopa ofalitsa ambiri sangathenso kupereka ndalama zawo ku Nyumba ya Ufumu ya m’dera lawo choncho anasankha kuti mwezi uliwonse, ku akaunti yawo ya kubanki kuzichotsedwa ndalama zawo zina kuti ziziperekedwa pa donate.pr418.com. Mlongo wina wa ku United States wazaka 74 dzina lake Susan Cohen, amagwiritsa ntchito njira imeneyi. Iye anati: “N’zosavuta, ngati ine ndikukwanitsa, aliyense akhoza kukwanitsa. Ndikusangalala kwambiri kudziwa kuti zopereka zanga zikuthandizira pa ntchito yolalikira padziko lonse.”
M’bale Eduardo Paiva yemwe amakhala ku Brazil, poyamba ankaganiza kuti kupereka kudzera pa donate.pr418.com yangokhala njira inanso yowonjezera ngati munthu sanathe kupereka ndalama zake ku Nyumba ya Ufumu. Iye anati: “Posachedwapa, ndazindikira kuti imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yomwe tingagwiritse ntchito popitiriza kuthandiza nawo pa ntchito yapadziko lonse pamene kwagwa mavuto adzidzidzi. Tikhoza kugwiritsa ntchito njirayi posonyeza chikondi komanso mtima woyamikira m’masiku otsirizawa.”
M’bale Gajus Glockentin, yemwe amayang’anira Ofesi Yoona za Ndalama kulikulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova mumzinda wa Warwick, New York, anati: “N’zolimbitsa chikhulupiriro kuona mtima umene abale ali nawo wofuna kuthandiza pa ntchito yolalikira. Tikuyamikira kwambiri zopereka zimenezi. Tikuyesetsa kuonanso zimene tingachite kuti tichepetse ndalama zimene timagwiritsa ntchito padziko lonse n’cholinga choti zopereka zizigwiritsidwa ntchito m’njira yabwino kwambiri. Ngakhale kuti anthu ena akufunikira kuchepetsa ndalama zimene amapereka, iwo adakali ndi mtima wofuna kuthandiza gulu la Yehova.”—2 Akorinto 9:7.