Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale ndi alongo a ku Ukraine akusamukira kumayiko ena

9 JUNE, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Abale ndi Alongo Omwe Anathawa ku Ukraine Ayamba Moyo Watsopano Kumayiko Ena

Abale ndi Alongo Omwe Anathawa ku Ukraine Ayamba Moyo Watsopano Kumayiko Ena

Iryna Makukha, tsopano akukhala m’dziko la Czech Republic

Nkhondo itangoyamba ku Ukraine, Mlongo Iryna Makukha yemwe ali ndi zaka 46, anathamangira kusiteshoni yasitima ku Kharkiv. Iye anaona kuti angakhale wotetezeka ngati atatuluka m’dziko la Ukraine. Zinthu zitafika poipa, anthu ankangokwerapo sitima iliyonse osadziwa komwe akulowera. Sitima yomwe anakwera Mlongo Makukha inanyamuka pasiteshoni mawindo ake ali otchinga pofuna kuteteza anthu kuti asavulazidwe. Ulendo uli mkati m’pamene mlongoyu anadziwa kuti sitimayo inkapita ku Slovakia.

Tsopano Mlongo Makukha amakhala m’dziko la Czech Republic ndipo anafika ku Prague lomwe ndi likulu la dzikolo pa 3 March, 2022. Iye anayamba kugwira ntchito ya m’nyumba ndipo amakhala nyumba imodzi ndi alongo enanso awiri omwe anathawa nkhondo ku Ukraine. Mlongoyu akuphunzira kulankhula Chicheki ndipo anayambiranso kuchita utumiki wanthawi zonse womwe wakhala akuchita kwa zaka 20.

Mlongo Makukha ananena kuti: “Ndadzionera ndekha ndi maso angawa mmene Yehova amatisamalirira pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu. Zimenezi zalimbitsa kwambiri chikhulupiriro changa.”

Abale ndi alongo pafupifupi 23,000, anasankha kuthawira kumayiko ena. Omwe anasankha kuthawa, tsopano ndi otetezeka. Koma ayenera kupeza ntchito, malo okhala, kukhala ndi zikalata zowalola kukhala m’dzikolo, kuyambitsa ana awo sukulu zatsopano kwinaku akuphunzira chilankhulo china. Abale ndi alongowa amaona kuti kutumikira Yehova komanso Akhristu anzawo n’zomwe zikuwathandiza pa nthawi yovutayi.

Anatoli, Olena ndi Alina Perceac akukhala m’dziko la Romania

M’bale Anatoli Perceac ndi mkazi wake Olena komanso mwana wawo wamkazi Alina wazaka 17, anayamba moyo watsopano m’dziko la Romania. Iwo ankakhala ku Mykolaiv Oblast ku Ukraine ndipo mabomba anawononga nyumba zambiri m’derali. Banjali linasamuka pa 6 March, 2022. Chifukwa chakuti M’bale Perceac ndi nzika ya ku Moldova, analoledwa kuti asamukire ku Romania limodzi ndi banja lake. Mlongo Olena Perceac anafotokoza mmene zimakhalira munthu akasamukira dziko lina. Iye anati zimakhala ngati “kuzula mtengo ndi mizu yake yomwe n’kukaudzala malo ena.”

Mothandizidwa ndi abale a ku Romania, banja la M’bale Perceac linapeza nyumba yokhala. Kuwonjezera apo, m’bale ndi mlongo Perceac anapeza ntchito ndipo mwana wawo Alina amakwanitsa kuphunzira kusukulu yake ya ku Ukraine kudzera pa intaneti.

Abale ndi alongo a ku Romania akuthandiza banjali kupeza zinthu zofunika komanso akulilimbikitsa mwauzimu. Abale ndi alongo amakonda kucheza ndi banjali kuti asamadzione kuti ali okhaokha kudziko lachilendo. Mlongo Perceac ndi Alina akuphunzira Chiromaniya pogwiritsa ntchito apu ya JW Language komanso polowa muutumiki limodzi ndi abale ndi alongo amumpingo wawo watsopano. M’bale Perceac anakula akulankhula Chiromaniya.

M’baleyu ananena kuti: “Takhala tikuona Yehova akutithandiza kuyambira pachiyambi. Taona chikondi cha Yehova kudzera m’gululi komanso poona mmene abale ndi alongo athu akutithandizira.”

Vladyslav Havryliuk ndi mayi ake Alina Havryliuk, tsopano ali m’dziko la Poland

Mwamuna wa Mlongo Alina Havryliuk anamwalira nkhondo isanayambe. Iye limodzi ndi mwana wake wamwamuna wazaka 16 dzina lake Vladyslav, anafika ku Suwałki m’dziko la Poland kuchokera ku Vinnystia m’dziko la Ukraine pa 27 February. Mlongoyu ananena kuti: “Poyamba ndinali ndi nkhawa kuti ndikakhala kuti ndi mwana wanga komanso kuti tidzapeza bwanji zinthu zofunika. Komabe ndinali ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzatisamalira.”

Mlongo Alina Havryliuk ali ndi zaka 37. Atangofika ku Poland, anayamba kufufuza ntchito yomwe ingathe kumamupatsa mpata wopezeka kumisonkhano. Anapeza ntchito yosamalira ana komanso kukonza m’makalasi pa sukulu ina. Mlongoyu ananena kuti: “Chofunika kwambiri n’chakuti ntchitoyi imandipatsa mpata wolowa muutumiki komanso kupeza zinthu zofunika.”

Mlongoyu ndi mwana wake Vladyslav, akuphunzira Chipolishi ndipo akuchita upainiya wothandiza wopitirira mumpingo wachipolishi. Vladyslav anayamba kuphunzira pasukulu ina yasekondale.

Abale ndi alongo athu a ku Ukraine akukumana ndi mavuto ambiri komanso kusintha kwa zinthu zina pa moyo wawo. Komabe Yehova akupitiriza kuwapatsa mphamvu zoposa zachibadwa. Iwo akuona kuti mawu opezeka pa 2 Akorinto 4:8 ndi oona. Omwe amati: “Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.”