Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Emilia wa ku Switzerland

APRIL 15, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Achinyamata a Mboni Apeza Njira Zina Zolalikirira pa Nthawi ya Mliri

Achinyamata a Mboni Apeza Njira Zina Zolalikirira pa Nthawi ya Mliri

Achinyamata a Mboni padziko lonse akupitirizabe kuchita zinthu zokhudza kulambira poyesetsa kupeza njira zina zolalikirira komanso kulimbikitsa abale ndi alongo awo pa nthawi ya mliriyi.

Ku New Zealand, anthu amakonda kuika matoyi, zidole ndi zithunzi m’mawindo n’cholinga choti ana akamadutsa aziona. Achinyamata a m’mipingo yosiyanasiyana anaona kuti akhoza kugwiritsanso ntchito njira imeneyi polalikira ndipo anapanga zithunzi za Kalebe ndi Sofiya, n’kulembapo kuti, “Onerani mavidiyo athu pa jw.org.”

Zithunzi za Kalebe ndi Sofiya zaikidwa pawindo ku New Zealand

Emilia wa ku Switzerland, wazaka 9, ali ndi vuto la kuchepa kwa chitetezo m’thupi. Iye analembera makalata anthu omwe amakhala m’nyumba zosamalirako okalamba, komwe panopa palibe akuloledwa kupitako. M’makalatawo anaikamonso chithunzi cha Nowa ndi chingalawa zomwe anajambula. Emilia anafotokoza kuti nthawi ina nayenso Nowa ndi banja lake anakhala paokha ndipo ndi zomwe zinawapulumutsa. Emilia analimbikitsa anthu okalamba okhala m’nyumbazi kuti “asatuluke, akhale ngati Nowa.” Mliriwu ukatha, Emilia akufuna kuonana pamasom’pamaso ndi anthuwo.

Anthu anachita chidwi ndi makalata a Emilia moti anamuyankha ndipo nayenso anawalembera ena mwa anthuwo makalata enanso. Mtolankhani wina wam’deralo anamva zomwe Emilia anachitazi ndipo analemba nkhani yake mu nyuzipepala.

Banja la a Kempf ku Canada

Alongo awiri achitsikana, Peyton ndi Ella Kempf a ku Ontario, ku Canada, akuyesetsa kulumikizana ndi abale ndi alongo amumpingo pa nthawi ya mliriwu. Bambo awo a Jared anafotokoza kuti: “Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, ana athu anatithandiza kukonza mndandanda wa anthu omwe tinkafuna kulankhula nawo.” A Jessica, mayi wa anawa, ananenanso kuti: “Tikufuna kuwaphunzitsa atsikanawa kudziwa kufunika kolumikizana ndi abale ndi alongo athu, achibale kuphatikizaponso anzathu kuti azidzimva kuti sitinawaiwale.”

Stella wa ku United States

Ku Colorado, U.S.A., nayenso mtsikana wazaka 9 dzina lake Stella ndi mayi ake anakonza zoti azilankhulana ndi abale ndi alongo amumpingo wawo. Analemba mndandanda wa anthu ndipo anaimbira foni wina aliyense payekha.

Abale awiri, Jonathan ndi Sean McKampson, azaka 12 ndi 15, amatumikira mumpingo wa chinenero cha Chitchainizi limodzi ndi makolo awo ku Arizona. Iwo akupitirizabe kulalikira polemba makalata mu Chitchainizi m’mawa uliwonse asanayambe kuphunzira zakusukulu. Popeza kuti akuphunzirabe chinenerochi, akumafunika nthawi yambiri komanso khama kuti amalize kulemba makalatawa. Ngakhale zili choncho, abalewa akuyesetsa kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu olankhula Chitchainizi.

Jonathan ndi Sean a ku United States

Ana 6 azaka zapakati pa ziwiri mpaka 15, mayi awo limodzi ndi mlongo wina yemwe ndi mpainiya, ankakonda kukalalikira kumalo ena osamalirako okalamba chakumadzulo kwa Michigan. Koma chifukwa cha mliri wa kolonavairasi, akuluakulu aboma analetsa kufika kumalowa. Panopa makolo a anawa amangojambula nyimbo za Ufumu zomwe anawo amaimba kapenanso kuwerengedwa kwa mavesi m’Baibulo, n’kutumizira okalamba omwe amakhala kumalowa. Mmodzi wa ogwira ntchito kumalo osamalira okalambawa anauza bambo wa anawa kuti, imodzi mwa mavidiyo omwe anatumiza inathandiza wokalamba wina kuti mtima wake ukhale m’malo chifukwa anali ndi nkhawa kwambiri atamvetsera nkhani zokhudza anthu amene amwalira ndi mliri wa kolonavairasi.

Sitikukayikira kuti Yehova akusangalala kwambiri ndi khama lomwe achinyamatawa akuchita posonyeza kukonda ena komanso kumutamanda pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira.—Salimo 148:12, 13.