Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 3, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Akuluakulu a Boma Anayamikira Ntchito Yapadera Yolalikira za Ufumu mu 2020

Akuluakulu a Boma Anayamikira Ntchito Yapadera Yolalikira za Ufumu mu 2020

M’mwezi wa November a Mboni za Yehova padziko lonse anagwira ntchito yogawira magazini ya Nsanja ya Olonda Na. 2 2020 kwa anthu ochita bizinesi, achibale awo ndiponso anthu ena achidwi. Chosangalatsa kwambiri ndi ntchito yapaderayi ndi chakuti akuluakulu a boma am’mayiko osiyanasiyana analandira nawo magaziniyi. Maofesi a Nthambi ayamba kale kulandira malipoti ambirimbiri osangalatsa.

Ku Sierra Leone, a Rex Bhonapha omwe ndi Wachiwiri kwa Nduna Yoona za Malo, Nyumba ndi Chitukuko cha m’Mizinda analemba kalata yothokoza abale chifukwa chowatumizira magaziniyi. Iwo anawonjezera kuti: “Ndisaname magaziniyi yandithandiza ndiponso yandiphunzitsa zambiri. Panopa ndikumaiwerenga tsiku lililonse.”

Ku Samoa, Nduna Yaikulu ya m’dzikolo inalembera kalata abale yowayamikira ndi kuwauza kuti imaona kuti Pemphero la Ambuye ndi lofunika kwambiri. Komanso Pulezidenti wa dzikolo dzina lake Tuimalealiifano Vaaletoa Sualauvi II, ananena kuti amayamikira kwambiri chifukwa cha ntchito yophunzitsa Baibulo imene timagwira. Iye ananena kuti ntchitoyi “ikuthandiza anthu komanso ikuwaphunzitsa zambiri zokhudza Baibulo n’cholinga choti asinthe moyo wawo.” Anayamikiranso abale chifukwa choimitsa kaye misonkhano yomwe amakhala nayo ku Nyumba ya Ufumu komanso kulalikira kunyumba ndi nyumba chifukwa cha mliri wa COVID-19.

A Osvaldo Cartagena García, omwe ndi mlembi wa boma ku Chile ananena kuti: “Ndikukhulupirira kuti akuluakulu a boma m’dziko lathu aphunzirapo kanthu pa ntchito yapadera yomwe mwagwira ndipo iwalimbikitsa kuti nawonso azichitira zinthu zabwino anthu a m’dzikoli, makamaka tikaona zimene zikuchitika m’dziko lathu panopa komanso padziko lonse lapansi.”

Phungu wina wa nyumba yamalamulo ku Germany dzina lake Deutscher Bundestag analembera ofesi ya nthambi ya Central Europe yomwe ili ku Germany kuti: “Chipembedzo chanu ndimachidziwa bwino. Anthu inu ndimakutayirani kamtengo chifukwa mumauza anthu molimba mtima kuti ndinu a Mboni za Yehova. . . . Ndikudziwanso kuti chipembedzo chanu ndi chimene chinazunzidwa kwambiri pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi.”

Komanso unduna wina wa boma la Germany unathokoza a Mboni za Yehova chifukwa chotonthoza anthu pa nthawi ya mliri wa COVID-19. A ku undunawu anati: “Mukamatonthoza anthu mumayesetsa kuwathandiza kuti azichita zinthu mogwirizana m’dziko lathu.”

Ku Colombia akuluakulu a boma awiri analembera kalata ofesi ya nthambi yothokoza chifukwa chowapatsa magaziniyi ndipo ananena kuti agawiranso anthu ena. Bwana wina wa ku Unduna wa Zachilengedwe ndi Chitukuko Chokhazikika analemba kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa chonditumizira magazini ya Nsanja ya Olonda chifukwa ili ndi uthenga wopulumutsa moyo.”

A Frank Okyere omwe ndi kazembe wa dziko la Ghana ku Japan anafotokoza kuti: “Ndikuona kuti magaziniyi ndi yothandiza kwambiri chifukwa ili ndi njira zosiyanasiyana zimene zingathandize anthu polimbana ndi mavuto amene amakumana nawo.”

Nayenso kazembe wochokera ku Azerbaijan anati: “Zikomo kwambiri potumiza magazini ya Nsanja ya Olonda yapaderayi ku maofesi athu. Ineyo ndasangalala kwambiri kuiwerenga.”

Tonsefe tikugwirizana ndi zimene M’bale Amaro Teixeira ananena. M’baleyu amayang’anira Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku nthambi ya ku Mozambique. Iye anati: “Sitinkayembekezera kuti ntchito yapaderayi ithandiza anthu ambiri chonchi. Takwanitsa kuuza uthenga wa Ufumu anthu amene poyamba zinali zovuta kuti tiwafikire.”

Sitikukayikira kuti tipitirizabe kulandira mauthenga oyamikira kuchokera kwa akuluakulu a boma komanso anthu ena pamene tikupitirizabe kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa “anthu onse apamwamba.”—1 Timoteyo 2:2.