Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Venezuela: Mlongo akuwerenga pojambula nkhani m’chinenero cha Chiwarao (pamwamba kumanzere) ndiponso abale awiri omwe amamasulira m’Chipiaroa ali mkati mogwira ntchito (pansi kumanzere). South Korea: Banja likuonera msonkhano wa 2020 (kumanja)

SEPTEMBER 4, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Anakwanitsa Kumasulira Msonkhano wa 2020 Ngakhale Panali Mavuto

Anakwanitsa Kumasulira Msonkhano wa 2020 Ngakhale Panali Mavuto

Msonkhano wa 2020 wakuti “Kondwerani Nthawi Zonse,” unali wapadera kwambiri m’mbiri yamasiku ano ya Mboni za Yehova. Nkhani zapamsonkhanowu zinamasuliridwa m’zinenero zoposa 500 ndipo unali wochita kujambulidwa. Omasulira anakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kuperewera kwa zipangizo komanso kuchepa kwa nthawi.

Mmodzi wa anthu omasulira Chikikuyu ku Kenya anati: “Popeza kuti nthambi inatsekedwa chifukwa cha mliri wa COVID-19, tinali ndi anthu ochepa omwe akanatha kuwerenga kusitudiyo. Tinathana ndi vuto limeneli pogwiritsa ntchito abale ndi alongo omwe sanali pa nthambi. Tikuona kuti ndife amwayi kwambiri chifukwa chakuti taona mzimu wa Yehova ukugwira ntchito.”

Omasulira m’Chinenero Chamanja cha ku Korea komanso omasulira m’Chikoreya anakumananso ndi mavuto ofanana ndi amenewa. Abale ochita kuyendera omwe amagwira nawo ntchito yomasulira sakanatha kupita ku Beteli kuti akawerenge nkhani kusitudiyo.

M’bale akugwiritsa ntchito chipinda china m’nyumba mwake ngati situdiyo pojambula nkhani ndi mavidiyo m’Chinenero Chamanja cha ku Korea

Kuti athane ndi vuto limeneli abale ena anasintha zipinda zina m’nyumba zawo kuti zikhale masitudiyo. Abale m’mipingo ndi amene anapereka zambiri mwa zipangizo zojambulira. Komanso popeza kuti misonkhano yonse inaimitsidwa kaye, ofesi ya nthambi inatha kugwiritsa ntchito makamera ena omwe anali m’Malo a Misonkhano pojambula nkhani m’Chinenero Chamanja.

Ku Venezuela, omasulira ena ankalimbana ndi mavuto a intaneti. Ena analibe zida zokwanira zogwiritsa ntchito. Komabe, omasulirawa anayesetsa kugwiritsa ntchito zilizonse zimene akanatha kuti akwaniritse ntchito yawo. Mwachitsanzo, m’dera lina omasulira anagwiritsa ntchito matiresi kuti achepetse phokoso pojambula nkhani.

Mumzinda wa Juba ku South Sudan, muli abale amene amamasulira nkhani m’Chizande. Mmodzi wa omasulirawa anati: “Nditamva kuti tijambula msonkhano wonse, ndinaganiza kuti, ‘Sizingatheke. N’zosatheka kujambula msonkhano wonse wokhala ndi mbali zoposa 90 za mawu ndi mavidiyo pa miyezi iwiri yokha.’ Koma panopa pambuyo poona kuti zimenezi zinatheka, ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake. Iye amachita zinthu m’njira yodabwitsa kwambiri.”—Mateyu 19:26.

Msonkhano wa 2020 wakuti “Kondwerani Nthawi Zonse,” unalidi mphatso yapadera yochokera kwa Yehova, “amene chifuniro chake n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Timoteyo 2:4.