21 APRIL, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Anthu Mamiliyoni Anachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu
Pa 15 April 2022, a Mboni za Yehova padziko lonse limodzi ndi anthu omwe anawaitana, anachita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Aka kanali koyamba kuchita mwambo wofunikawu pamasom’pamaso kuchokera mu 2019. Omwe sanakwanitse kupita kumalo omwe kunkachitikira mwambowu, analumikizidwa kudzera pa zipangizo zamakono.
A Mboni za Yehova amaona kuti mwambo wapachakawu Wokumbukira Imfa ya Khristu, ndi wofunika kwambiri. Chifukwa cha mliri kwa COVID-19, zaka ziwiri zapitazi, mwambowu unachitika kudzera pa vidiyokomfelensi. Anthu oposa 21 miliyoni anapezeka pa Chikumbutso mu 2021.
Kwa anthu ena ngati Markensia Remy wa ku Haiti, kanali koyamba kuti apezeke pamwambowu pamasom’pamaso. Tsopano Markensia watha chaka kuchokera pomwe anabatizidwa. Iye ananena kuti: “Ndasangalala kwambiri kuti ndapezeka nawo pa Chikumbutso cha pa Nyumba ya Ufumu ndipo sindikudziwa kuti ndingafotokoze bwanji mmene ndasangalalira. Ndikuona kuti ndili m’banja labwino kwambiri.”
Tikuthokoza kwambiri chifukwa chokhala ndi mwayi wochita Mwambo wa Chikumbutso chaka chino. Tikuthokozanso kwambiri Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu, chifukwa chachikondi chachikulu kwambiri chomwe anatisonyeza.—Yohane 3:16.
Argentina
Bolivia
Brazil
Cambodia
Central African Republic
Cook Islands (Rarotonga)
Ecuador
Indonesia
Israel
Japan
Kazakhstan
Kosovo
Mexico
Paraguay
Peru
Philippines
Poland
Romania
Spain
Taiwan
Ukraine
United States
Venezuela