Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

17 JUNE 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Baibulo la Dziko Latsopano la Chitajiki Linatulutsidwa pa Msonkhano Wochita Kujambula

Baibulo la Dziko Latsopano la Chitajiki Linatulutsidwa pa Msonkhano Wochita Kujambula

Pa 13 June, 2021, M’bale Mark Sanderson, wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Opatulika mu Chitajiki. Baibuloli linatulutsidwa pa msonkhano wochita kujambula.

Mfundo Zokhudza Ntchito Yomasulira

  • Chitajiki chimalankhulidwa ndi anthu pafupifupi 14 miliyoni ndipo zikuoneka kuti pa anthu amenewa, anthu pafupifupi 5miliyoni amakhala ku Tajikistan

  • Omasulira ochokera m’mayiko osiyanasiyana anagwira ntchitoyi ndipo inawatengera zaka 4 kuti aimalize

Mmodzi mwa omasulirawo anati: “Baibulo la Dziko Latsopano la Chitajiki lithandiza anthu owerenga kuti azimva mosavuta tanthauzo la zimene akuwerenga komanso mmene angazigwiritsire ntchito. Sitikukayikira kuti lithandiza anthu onse kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova yemwe ndi Mlembi wa Baibulo.”—Yakobo 4:8.