Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

17 JUNE, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Buku Lofufuzira Nkhani la pa JW Library Aliwonjezera Kalozera wa Malemba

Buku Lofufuzira Nkhani la pa JW Library Aliwonjezera Kalozera wa Malemba

Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani linakonzedwanso ndipo linayamba kupezeka pa apu ya JW Library pa 25 April 2022. Tsopano bukuli lili ndi mndandanda waukulu wa malifalensi ofotokozera malemba.

N’chiyani Chomwe Chasintha M’bukuli?

Kungoyambira pomwe bukuli linatulutsidwa mu 2013, Buku Lofufuzira Nkhani lakhala likupezeka ndi kalozera wa malemba wa malifalensi a mabuku athu am’mbuyo.

M’zaka zaposachedwapa, takhala tikuwonjezera mabuku athu akale mu apu ya JW Library. Mabuku ambiri omwe ankapezeka pa Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI, tsopano ayambanso kupezeka mu apu ya JW Library. M’Buku Lofufuzira Nkhani lomwe langokonzedwali, mukupezeka mabuku athu akale kuphatikizaponso buku la Insight on the Scriptures. (M’Buku Lofufuzira Nkhani la Chingelezi) Mu Buku Lofufuzira Nkhani la pa JW Library, mukupezakanso mawu a m’malifalensi onse. Choncho mukhoza kuwona zomwe zili mu lifalensi iliyonse ngakhale kuti simunalowe pa intaneti.

M’bukuli mukupezekanso malifalensi a maphunziro a m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Mlongo wina dzina lake Kari ananena kuti: “Ndinkachita mantha kuti ndilalikire pa foni, komabe ndinkadziwa kuti anthu akufunitsitsa kutonthozedwa. Nthawi zina ndimatha kukumbukira malemba, komabe ndimafunitsitsa nditamafotokoza malembawo m’njira yosavuta komanso yomwe ingathe kufika munthuyo pamtima kuti tipitirize kukambirana. Ndimasangalala kwambiri komanso sindimadzikayira ndikakhala mu utumiki chifukwa ndikangotsegula lemba, nthawi yomweyo ndimapeza malifalensi m’Buku Lofufuzira Nkhani komanso ndimapeza maphunziro a m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.

Njira zokonzera Buku Lofufuzira Nkhani zafewetsedwa kuti bukuli lizipezeka m’zilankhulo zinanso zambiri. Ivo yemwe amatumikira ku nthambi ya Chile ananena kuti: “Aka ndi koyamba kuti tikhale ndi Buku Lofufuzira Nkhani mu Chimapudunguni. Sindinagwirepo ntchito yokonza buku ngati limeneli, koma ntchito yake inali yophweka. Abale anadabwa kwambiri kuona bukuli m’chilankhulo chathu. Iwo sankaganizako n’komwe kuti bukuli lingapezeke mu Chimapudunguni chifukwa chilankhulochi chimangolankhulidwa ndi anthu ochepa. Komabe, anasangalala kwambiri kulandira bukuli chifukwa ndi lothandiza kwambiri ukamaphunzira pawekha, kukonzekera ndemanga komanso nkhani.”

Kodi Mungagwiritse Ntchito Bwanji Kalozera wa Malemba wa mu Buku Lofufuzira Nkhani?

  • Mukatsegula Baibulo, pitani pa vesi lomwe mukufuna kufufuzalo.

  • Kenako, dinani nambala ya vesilo. Pakatuluka chithunzi cha zizindikiro, dinani chizindikiro cha Buku Lofufuzira Nkhani. Ngati chizindikirocho sichikuoneka, ndiye kuti palibe malifalensi a mu Buku Lofufuzira Nkhani ofotokozera vesilo.

Mabuku omwe angotuluka chaposachedwa, amaikidwa koyambirira pa mndandanda wa malifalensi a mu Buku Lofufuzira Nkhani. Ngati mukufuna lifalensi yakale, tsikani m’munsi mwa mndandanda wa malifalensiwo. Ponena za mavesi a m’Baibulo omwe tinasintha kafotokozedwe, malifalensi atsopanowa amakhala ndi mfundo zatsopano zomwe tikuyendera.