23 JANUARY 2024
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
“Chilichonsetu Nʼchotheka kwa Munthu Amene Ali Ndi Chikhulupiriro”
Posachedwapa khoti la m’boma la Nakhimovskiy mumzinda wa Sevastopol lilengeza chigamulo chake, pa mlandu wokhudza M’bale Maksim Zinchenko. Loya woimira boma pamlanduwu akuyembekezereka kunena chilango chimene akufuna kuti M’bale Zinchenko apatsidwe.
Zokhudza M’baleyu
Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzadalitsa M’bale Maksim ndi ena onse amene akupitiriza kuchita chifuniro chake chifukwa cha kulimba mtima komanso kupirira kwawo.—Aheberi 10:35, 36.
Nthawi ndi Zochitika
17 May 2023
Anapezedwa ndi mlandu wochita zinthu ndi gulu lopereka chiopsezo ku boma
22 May 2023
Anakachita chipikisheni m’nyumba yawo. M’bale Maksim ndi mkazi wake Karina anafunsidwa mafunso. M’bale Maksim anasungidwa m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu
24 May 2023
M’bale Maksim anatulutsidwa m’ndende koma anaikidwa pa ukadi wapakhomo
12 July 2023
Mlandu unayamba kuzengedwa m’khoti