Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Artem Shabliy

1 APRIL, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Chitetezo Cha Yehova Chili Ngati ‘Khoma la Mwala’

Chitetezo Cha Yehova Chili Ngati ‘Khoma la Mwala’

Pa 16 February 2022, khoti la Mzinda wa Kerch m’Dziko la Crimea linapeza kuti M’bale Artem Shabliy ndi wolakwa ndipo anamulamula kuti asapalamulenso mlandu uliwonse kwa zaka ziwiri. M’bale Artem Shabliy sakuyenera kupita kundende panopo.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 26 May, 2020

    Apolisi anakafufuza zinthu kunyumba kwa M’bale Shabliy komanso kunyumba zamabanja ena a Mboni za Yehova zokwana 4. Pa nthawiyo, mwana wamwamuna wazaka 4 wa M’bale Shabliy, magalasi anamucheka m’miyendo, apolisi ataphwanya windo la nyumba yawo. Pambuyo pa maola atatu omwe apolisi ankafufuza zinthu, anamanga M’bale Shabliy n’kukamutsekera m’chipinda chayekhayekha kwa masiku atatu

  2. 9 June, 2020

    M’bale Shabliy anapempha Khoti la Mzinda wa Kerch kuti limuonetse lipoti lomwe apolisi analemba lomwe lidzagwiritsidwe ntchito pomuzenga mlandu. Ngakhale kuti zinali zovomerezeka, koma khoti linakana kumuonetsa lipotilo

  3. 24 May, 2021

    Khoti linayamba kumvetsera mlandu. Abale ndi alongo ambiri anadzaza pakhoti kuti adzathandize abale awo komabe sanawalole kuti alowe m’khotimo

Zokhudza M’baleyu

Monga mmene M’bale Shabliy wafotokozera, Yehova amathandiza atumiki ake okhulupirika. Tili ndi chikhulupiriro kuti iye apitirizabe kukhala thanthwe komanso malo othawirako otetezeka kwa abale ndi alongo athu okondedwa a ku Crimea ndi ku Russia.—Salimo 18:2.