AUGUST 9, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Linagamula Mlandu Mokomera M’bale Rostom Aslanian
A Mboni za Yehova Awina Mlandu ku Transnistria
Pa 13 July 2021, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe (ECHR) linagamula kuti M’bale Rostom Aslanian ndi wosalakwa pa mlandu umene umakhudza mayiko a Moldova ndi Russia. M’bale Aslaniana anakasuma kuti anamulakwira pomugamula kuti akakhale kundende ku Transnistria (Pridnestrovskaia Moldavskaia Republic) atakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Kuwina kwa mlanduwu n’kothandiza kuti a Mboni za Yehova asadzazengedwenso mlandu wofanana ndi umenewu ku Transnistria.
Ngakhale kuti dera la Transnistria limadziwika kuti ndi mbali ya dziko la Moldova, nalonso dziko la Russia linapanga mgwirizano woti liziyang’anira nkhani zokhudza chitetezo cha m’derali. Mayiko onsewa ndi mamembala a mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe ndipo ayenera kulemekeza nkhani yokhudza ufulu wa munthu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Mu 2010, M’bale Aslanian anaikidwa pa mndandanda wa anthu oti akayambe usilikali koma iye anapempha kuti apatsidwe ntchito ina chifukwa cha zimene amakhulupirira kuchokera m’Baibulo. Pa 29 March 2011, pempho lakeli linakanidwa moti anamupeza kuti ndi wolakwa ndipo anamugamula kuti akakhale ku ndende chaka chimodzi. M’bale Aslanian anakhaladi ku ndende kwa chaka chathunthu koma patapita nthawi mlandu wake anaupititsa ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe.
Popereka chigamulo, a Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe, anaona kaye zigamulo zimene zinaperekedwapo m’mbuyomu pofuna kutsimikizira kuti M’bale Aslanian sanaphwanye lamulo lililonse kuti afike pomugamula kuti apite kundende chifukwa chokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. A Khoti atafufuza, anapeza kuti boma la Russia ndi lomwe linkayendetsa ntchito zokhudza usilikali, zachuma komanso zandale m’boma la Transnistria. Choncho zinadziwika kuti boma la Russia osati la Moldova, ndilimene linali ndi mlandu pa nkhani ya kumangidwa kwa M’bale Aslanian. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe, linagamula kuti aboma anaphwanyira M’bale Aslanian ufulu wachipembedzo pogamula kuti akakhale kundende chaka chimodzi ndipo anati pachifukwa chimenechi, boma la Russia limupatse chipukuta misozi.
Ndife osangalala kuti abale athu ku Transnistria ndiwotetezeka mwalamulo chifukwa cha chigamulo chimene chinaperekedwachi. Zimenezi zikutitsimikiziranso kuti Yehova akupitiriza kusonyeza anthu ake chikondi chokhulupirika komanso kuwasamalira akamazunzidwa.—Salimo 18:25.